Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 36:15 - Buku Lopatulika

15 Amenewa ndi mafumu a ana aamuna a Esau: ana aamuna a Elifazi woyamba wa Esau: mfumu Temani, mfumu Omara, mfumu Zefo, mfumu Kenazi,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Amenewa ndi mafumu a ana amuna a Esau: ana amuna a Elifazi woyamba wa Esau: mfumu Temani, mfumu Omara, mfumu Zefo, mfumu Kenazi,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Naŵa mafumu a zidzukulu za Esau. Mwa ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau, panali mafumu aŵa: Temani, Omara, Zefo, Kenazi,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Nawa mafumu a zidzukulu za Esau: Mwa ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau panali mafumu awa: Temani, Omari, Zefo, ndi Kenazi,

Onani mutuwo Koperani




Genesis 36:15
19 Mawu Ofanana  

Ana aamuna a Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibiyoni, mkazi wake wa Esau, ndi awa: ndipo iye anambalira Esau Yeusi, ndi Yalamu, ndi Kora.


mfumu Kora, mfumu Gatamu, mfumu Amaleke: amenewa ndi mafumu a kwa Elifazi m'dziko la Edomu: amenewa ndi ana aamuna a Ada.


Amenewa ndi ana aamuna a Oholibama mkazi wake wa Esau; mfumu Yeusi, mfumu Yalamu, mfumu Kora, amenewa ndi mafumu obadwa kwa Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mkazi wake wa Esau.


Ndipo Ada anambalira Esau Elifazi; ndipo Basemati anabala Reuwele;


Namwalira Yobabu; ndi Husamu wa ku dziko la Atemani anakhala mfumu m'malo mwake.


Atamva tsono mabwenzi atatu a Yobu za choipa ichi chonse chidamgwera, anadza, yense kuchokera kwao, Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, napangana kudzafika kumlirira ndi kumsangalatsa.


Mbeu zao zikhazikika pamodzi nao pankhope pao, ndi ana ao pamaso pao.


Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,


Ndapenya woipa, alikuopsa, natasa monga mtengo wauwisi wanzika.


Pamenepo mafumu a Edomu anadabwa; agwidwa nako kunthunthumira amphamvu a ku Mowabu; okhala mu Kanani onse asungunuka mtima.


Chifukwa chake tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Edomu; ndi zimene walingalirira okhala mu Temani, ndithu adzawakoka, ana aang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.


Za Edomu. Yehova wa makamu atero: Kodi mu Temani mulibenso nzeru? Kodi uphungu wawathera akuchenjera? Kodi nseru zao zatha psiti?


chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndidzatambasulira Edomu dzanja langa, ndi kulilikhira munthu ndi nyama, ndi kulisandutsa labwinja; kuyambira ku Temani mpaka Dedani adzagwa ndi lupanga.


koma ndidzatumiza moto pa Temani, udzanyeketsa nyumba zachifumu za Bozira.


Ndipo amuna anu amphamvu adzatenga nkhawa, Temani iwe, kuti onse aonongeke m'phiri la Edomu, ndi kuphedwa.


Mulungu anafuma ku Temani, ndi Woyerayo kuphiri la Parani. Ulemerero wake unaphimba miyamba, ndi dziko lapansi linadzala ndi kumlemekeza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa