Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 35:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo anafa Debora mlezi wa Rebeka, naikidwa kunsi kwa Betele, pansi pa mtengo wathundu; ndipo anatcha dzina lake Aloni-Bakuti.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo anafa Debora mlezi wa Rebeka, naikidwa kunsi kwa Betele, pansi pa mtengo wathundu; ndipo anatcha dzina lake Aloni-Bakuti.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Debora mlezi wa Rakele, adamwalira komweko, ndipo adaikidwa patsinde pa mtengo wathundu ku Beteleko. Motero malowo adatchedwa Mtengo Wamaliro.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Debora mlezi wa Rakele anamwalira komweko nayikidwa mʼmanda pansi pa mtengo wa thundu cha kumunsi kwa Beteli. Choncho panatchedwa Aloni-Bakuti (mtengo wamaliro).

Onani mutuwo Koperani




Genesis 35:8
7 Mawu Ofanana  

Ndipo anamlola Rebeka mlongo wao ndi mlezi wake, amuke pamodzi ndi mnyamata wake wa Abrahamu, ndi anthu ake.


anauka ngwazi zonse, nachotsa mtembo wa Saulo, ndi mitembo ya ana ake, nabwera nayo ku Yabesi, naika mafupa ao patsinde pa mtengo wathundu ku Yabesi, nasala masiku asanu ndi awiri.


Ndipo mthenga wa Yehova anakwera kuchokera ku Giligala kunka ku Bokimu. Ndipo anati, Ndinakukweretsani kuchokera ku Ejipito, ndi kulowetsa inu m'dziko limene ndinalumbirira makolo anu; ndipo ndinati, Sindidzathyola chipangano changa nanu ku nthawi yonse;


Potero analitcha dzina la malowo Bokimu: namphera Yehova nsembe pomwepo.


Ndipo anakhala patsinde pa mgwalangwa wa Debora pakati pa Rama ndi Betele ku mapiri a Efuremu; ndi ana a Israele anakwera kwa iye awaweruze.


Mukapitirira pamenepo tsono ndi kufika ku mtengo wathundu wa ku Tabori, kumeneko adzakomana nanu anthu atatu akukwera kwa Mulungu ku Betele, wina wonyamula anaambuzi atatu, wina mikate itatu, wina thumba la vinyo.


Natenga mafupa ao nawaika patsinde pa mtengo wa bwemba uli mu Yabesi, nasala kudya masiku asanu ndi awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa