Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 35:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo anapita ndipo kuopsa kwa Mulungu kudagwera mizinda yakuwazinga, ndipo sanalondole ana a Yakobo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo anapita ndipo kuopsa kwa Mulungu kudagwera midzi yakuwazinga, ndipo sanalondole ana a Yakobo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Pamene Yakobe ndi ana ake adachoka, anthu onse a mizinda yozungulira adachita mantha, motero sadaŵatsatire.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Pamenepo ananyamuka, ndipo mtima woopa Mulungu unagwera anthu onse a mʼmizinda yozungulira, kotero kuti palibe aliyense amene anatsatira banja la Yakobo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 35:5
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, Mwandisautsa ndi kundinukhitsa ine mwa anthu okhala m'dzikomu, mwa Akanani ndi mwa Aperizi; ndipo ine ndine wa anthu owerengeka, adzandisonkhanira ine ndi kundikantha: ndipo ndidzapasulidwa ine ndi a pa nyumba yanga.


Ndipo anampatsa Yakobo milungu yachilendo yonse inali m'manja mwao, ndi mphete zinali m'makutu mwao: ndipo Yakobo anazibisa pansi pa mtengo wathundu unali pa Sekemu.


Ndi Asa ndi anthu anali naye anawalondola mpaka ku Gerari, nagwa Akusi ambiri osalimbikanso mphamvu iwowa; pakuti anathyoledwa pamaso pa Yehova ndi ankhondo ake; ndipo anatenga zofunkha zambiri.


Ndipo anakantha mizinda yonse pozungulira pake pa Gerari; pakuti mantha ochokera kwa Yehova anawagwera; ndipo anafunkha m'mizinda monse, pakuti mudachuluka zofunkha m'menemo.


Ndipo kuopsa kwa Yehova kunagwera maufumu a maiko ozungulira Yuda; momwemo sanayambane ndi Yehosafati.


Sanalola munthu awasautse; ndipo anadzudzula mafumu chifukwa cha iwowa.


Pamenepa anaopaopatu, pakuti Mulungu ali mu mbadwo wa wolungama.


Ndidzatumiza kuopsa kwanga kukutsogolere, ndipo ndidzapirikitsa anthu onse amene udzafika kwao, ndipo ndidzachita kuti adani ako onse adzakuonetsa m'mbuyo mwao.


Pakuti ndidzaingitsa mitundu ya anthu pamaso pako, ndi kukulitsa malire ako; ndipo palibe munthu adzakhumba dziko lako, pakukwera iwe kudzaoneka pamaso pa Yehova Mulungu wako katatu chaka chimodzi.


Palibe munthu adzaima pamaso panu; Yehova Mulungu wanu adzanjenjemeretsa ndi kuopsa dziko lonse mudzapondapo, chifukwa cha inu, monga anenana ndi inu.


Tsiku lino ndiyamba kuopsetsa nawe ndi kuchititsa mantha nawe anthu a pansi pa thambo lonse, amene adzamva mbiri yako, nadzanjenjemera, nadzawawidwa chifukwa cha iwe.


Ndipo kunali, pamene mafumu onse a Aamori okhala tsidya la kumadzulo la Yordani, ndi mafumu onse a Akanani okhala ku nyanja anamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a Yordani pamaso pa ana a Israele mpaka titaoloka, mtima wao unasungunuka, analibenso moyo chifukwa cha ana a Israele.


Natenga ng'ombe ziwiri nazidula nthulinthuli, nazitumiza m'malire monse mwa Israele, ndi dzanja la mithenga, nati, Amene sakudza pambuyo pa Saulo ndi pa Samuele, adzatero nazo ng'ombe zake. Ndipo kuopsa kwa Yehova kunawagwera anthu, natuluka ngati munthu mmodzi.


Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; chomwecho kunali kunthunthumira kwakukulu koposa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa