Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 34:19 - Buku Lopatulika

19 Ndipo mnyamatayo sanachedwe kuchichita popeza anakondwera ndi mwana wake wamkazi wa Yakobo; ndipo iye anali wolemekezedwa woposa onse a pa banja la atate wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo mnyamatayo sanachedwe kuchichita popeza anakondwera ndi mwana wake wamkazi wa Yakobo; ndipo iye anali wolemekezedwa woposa onse a pa banga la atate wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Ndipo mnyamatayo adafulumira kuchita zimene zinkafunikazo, chifukwa choti adaamkonda kwambiri mwana wa Yakobeyo. Sekemu anali wotchuka kwambiri m'banja lakwaolo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Mnyamata uja amene anali wolemekezeka kwambiri pa banja lake lonse, sanachedwe kuchita mdulidwe popeza anamukonda kwambiri mwana wa Yakobo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 34:19
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anamtumikira zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele; koma zidamuonekera iye ngati masiku owerengeka chifukwa cha chikondi chimene anamkonda iye nacho.


Mau ao ndipo anakomera Hamori ndi Sekemu mwana wake wa Hamori.


Ndipo Hamori ndi Sekemu mwana wake anafika ku chipata cha mzinda wao, nalankhulana ndi anthu a mzinda wao, kuti,


ndipo ng'ombe zazikazi zoonda ndi za maonekedwe oipa zinadya ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zonenepa.


Ndipo Naamani kazembe wa khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu anali munthu womveka pamaso pa mbuyake, ndi waulemu; popeza mwa iye Yehova adapulumutsa Aaramu; ndiyenso ngwazi, koma wakhate.


Ndipo Yabezi analemekezedwa koposa abale ake; ndi make anamutcha dzina lake Yabezi, ndi kuti, Popeza ndambala mwaululu.


Undilembe pamtima pako, mokhoma chizindikiro, nundikhomenso chizindikiro pamkono pako; pakuti chikondi chilimba ngati imfa; njiru imangouma ngati manda: Kung'anima kwake ndi kung'anima kwa moto, ngati mphezi ya Yehova.


Chifukwa chake anthu anga amuka m'nsinga, chifukwa cha kusowa nzeru; ndi amuna ao olemekezeka ali ndi njala, ndi khamu lao lauma kukhosi.


Iwe sudzatchedwanso Wosiyidwa; dziko lako silidzatchedwanso Bwinja; koma iwe udzatchedwa Hefiziba ndi dziko lako Beula; pakuti Yehova akondwera mwa iwe, ndipo dziko lako lidzakwatiwa.


Koma Balaki anaonjeza kutumanso akalonga, ochuluka, ndi omveka koposa awa.


Koma Ayuda anakakamiza akazi opembedza ndi omveka, ndi akulu a mzindawo, nawautsira chizunzo Paulo ndi Barnabasi, ndipo anawapirikitsa iwo m'malire ao.


Ndipo ambiri a iwo anakhulupirira; ndi akazi a Chigriki omveka, ndi amuna, osati owerengeka.


Ndipo Ahimeleki anayankha mfumu, nati, Ndipo ndani mwa anyamata anu onse ali wokhulupirika ngati Davide amene, mkamwini wa mfumu; wakuyenda mu uphungu wanu, nalemekezeka m'nyumba mwanu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa