Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 31:48 - Buku Lopatulika

48 Ndipo Labani anati, Muluwu ndiwo mboni pakati pa ine ndi iwe lero. Chifukwa chake anatcha dzina lake, Galedi;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

48 Ndipo Labani anati, Muluwu ndiwo mboni pakati pa ine ndi iwe lero. Chifukwa chake anatcha dzina lake, Galedi;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

48 Pambuyo pake Labani adati, “Mulu wamiyalawu udzakhala chikumbutso kwa ine ndi iwe.” Nchifukwa chake malowo adaŵatcha Galedi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

48 Labani anati, “Mulu uwu ndi mboni pakati pa inu ndi ine lero.” Ndi chifukwa chake unatchedwa Galeeda.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 31:48
10 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Anaankhosa aakazi asanu ndi awiriwa uwalandire padzanja langa, kuti akhale mboni zanga, kuti ndakumba ine chitsime chimenechi.


Ndipo iye anatenga abale ake pamodzi naye, namlondola iye ulendo wa masiku asanu ndi awiri: nampeza iye paphiri la Giliyadi.


Kuyambira ku Aroere, ndiko kumphepete kwa mtsinje wa Arinoni, ndi kumudzi wokhala kumtsinje kufikira ku Giliyadi, kunalibe mzinda wakutitalikira malinga ake; Yehova Mulungu wathu anapereka yonse pamaso pathu.


Koma ndinapatsa Arubeni ndi Agadi kuyambira ku Giliyadi kufikira ku mtsinje wa Arinoni, pakati pa chigwa ndi malire ake, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni;


koma lidzakhala mboni pakati pa ife ndi inu, ndi pakati pa mibadwo yathu ya m'tsogolo, kuti tikachita ntchito ya Yehova pamaso pake ndi nsembe zathu zopsereza, ndi zophera, ndi zoyamika; kuti ana anu asanene ndi ana athu m'tsogolomo, Mulibe gawo ndi Yehova.


Chifukwa chake tinati, Kudzali, akadzatero kwa ife, kapena kwa mibadwo yathu m'tsogolomo, kuti tidzati, Tapenyani, chitsanzo cha guwa la nsembe la Yehova, chomanga makolo athu, si kufukizapo nsembe yopsereza ai, kapena nsembe yophera ai, koma ndilo mboni pakati pa ife ndi inu.


Ndipo ana a Rubeni ndi ana a Gadi analitcha guwa la nsembelo: Ndilo mboni pakati pa ife kuti Yehova ndiye Mulungu.


Ndipo Yoswa anati kwa anthu onse, Taonani, mwala uwu udzakhala mboni yotitsutsa; pakuti udamva mau onse a Yehova amene ananena kwa ife; ndipo udzakhala mboni yotsutsa inu, mungakanize Mulungu wanu.


Atafa iye, anauka Yairi Mgiliyadi, naweruza Israele zaka makumi awiri mphambu ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa