Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 31:43 - Buku Lopatulika

43 Ndipo Labani anayankha nati kwa Yakobo, Akaziwa ndiwo ana anga, anawa ndiwo ana anga, zowetazi ndizo zoweta zanga ndi zonse ulinkuziona ndizo zanga: nanga ndidzachitira ine chiyani lero kwa ana anga aakazi amenewa, kapena ana ao amene anabala?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

43 Ndipo Labani anayankha nati kwa Yakobo, Akaziwa ndiwo ana anga, anawa ndiwo ana anga, zowetazi ndizo zoweta zanga ndi zonse ulinkuziona ndizo zanga: nanga ndidzachitira ine chiyani lero kwa ana anga akazi amenewa, kapena ana ao amene anabala?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

43 Labani adayankha Yakobe kuti, “Ana aakaziŵa ndi anga, ana ao ndi anga, pamodzi ndi zoŵeta zomwezi. Zonse ukuziwonazi nzanga. Koma tsopano ndiŵachitire chiyani ana anga aakaziŵa pamodzi ndi ana aoŵa?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

43 Labani anayankha Yakobo nati, “Ana aakaziwa ndi anga, ana awo ndi anganso. Ziwetozi ndi zanga. Chilichonse ukuona apa ndi changa. Koma tsopano ndingachite chiyani ndi ana anga aakaziwa kapena ndi ana awo?

Onani mutuwo Koperani




Genesis 31:43
3 Mawu Ofanana  

Ndipo anamva mau a ana ake a Labani kuti, Yakobo watenga zonse za atate wathu; m'zinthu zinali za atate wathu wapeza iye chuma ichi chonse.


M'mamawa Labani anauka nampsompsona ana ake aamuna ndi aakazi, nawadalitsa: ndipo Labani anachoka, nabwera kumalo kwake.


Ndipo ana aamuna ake onse ndi ana aakazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndilinkulirabe. Atate wake ndipo anamlirira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa