Genesis 31:39 - Buku Lopatulika39 Chimene chinazomoledwa ndi chilombo sindinachitengere kwa iwe; ndekha ndinalipira; padzanja langa unachifuna, chingakhale chobedwa kapena pausiku kapena pausana. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201439 Chimene chinazomoledwa ndi chilombo sindinachitengere kwa iwe; ndekha ndinalipira; pa dzanja langa unachifuna, chingakhale chobedwa kapena pausiku kapena pausana. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa39 Nkhosa ikajiwa ndi zilombo, ine ndinkalipira nthaŵi zonse, sindinkabwera nayo kwa inu, kuwonetsa kuti sindidalakwe. Munkafuna kuti ndilipire chilichonse chobedwa usiku kapena usana. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero39 Chiweto chikakhadzulidwa ndi chirombo, sindinkabwera nacho kwa inu. Ineyo ndinkalipira. Inuyo munkandilipiritsa kalikonse kobedwa masana kapena usiku. Onani mutuwo |