Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 31:32 - Buku Lopatulika

32 Aliyense umpeza ali nayo milungu yako, asakhale ndi moyo: pamaso pa abale athu, tayang'anira zako zili ndi ine, nuzitenge wekha. Pakuti sanadziwe Yakobo kuti Rakele anaiba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Aliyense umpeza ali nayo milungu yako, asakhale ndi moyo: pamaso pa abale athu, tayang'anira zako zili ndi ine, nuzitenge wekha. Pakuti sanadziwe Yakobo kuti Rakele anaiba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Koma mukapeza kuti wina aliyense pano ali ndi timilungu tanu, aphedwe ameneyo. Anthu tili nawoŵa akhale mboni pano pamene inu muyang'ane zinthu zanu m'katundu yenseyu. Tsono mukazipeza zanuzo mutenge.” Monsemo nkuti Yakobe ali wosadziŵa kuti Rakele adaaba timilunguto.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Koma mukapeza wina aliyense ndi milungu yanu, ameneyo sakhala ndi moyo. Anthu onse akupenya, lozani chilichonse chanu chimene chili ndi ine, ndipo ngati muchipeze tengani. Koma Yakobo sankadziwa kuti Rakele anabadi milunguyo.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 31:32
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu anati kwa Loti, Tisachite ndeu, ine ndi iwe, abusa anga ndi abusa ako: chifukwa kuti ife ndife abale.


Ndipo anati, Abale anga, musachitetu koipa kotere.


Chotero chilungamo changa chidzandivomereza m'tsogolo pamene udzandifika chifukwa cha malipiro amene ali patsogolo pako: iliyonse yosakhala yamathothomathotho ndi yamawangamawanga ya mbuzi, ndi iliyonse ya nkhosa yosakhala yakuda, ikapezedwa ndi ine, udzaiyesa yakuba.


Ndipo Labani ananka kukasenga nkhosa zake: ndipo Rakele anaba aterafi a atate wake.


Ndipo iye anatenga abale ake pamodzi naye, namlondola iye ulendo wa masiku asanu ndi awiri: nampeza iye paphiri la Giliyadi.


Tsono ungakhale ukadamuka chifukwa mtima wako ulinkukhumba nyumba ya atate wako, bwanji waba iwe milungu yanga?


Ndipo anayankha Yakobo nati kwa Labani, Chifukwa ndinaopa: chifukwa kuti, ndinati, Kapena udzandilanda ine ana ako aakazi.


Ndipo Labani analowa m'hema wa Yakobo, ndi m'hema wa Leya, ndi m'mahema a adzakazi awiri aja; koma sanapeze. Ndipo anatuluka m'hema wa Leya nalowa m'hema wa Rakele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa