Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 31:29 - Buku Lopatulika

29 M'dzanja langa muli mphamvu yakuchitira iwe zoipa koma Mulungu wa atate wako anati kwa ine usiku walero, kuti, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 M'dzanja langa muli mphamvu yakuchitira iwe zoipa koma Mulungu wa atate wako anati kwa ine usiku walero, kuti, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Ndili nazo mphamvu zakukuchita choipa. Koma usiku wapitawu, Mulungu wa atate ako wandiwuza kuti, ‘Usamuwopseze Yakobe mwa njira iliyonse.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Ndili nayo mphamvu yakukuchita choyipa; koma usiku wapitawu, Mulungu wa abambo ako wandiwuza ine kuti, ‘Usamuopseze Yakobo mwa njira iliyonse.’

Onani mutuwo Koperani




Genesis 31:29
19 Mawu Ofanana  

Ndipo anayankha Labani ndi Betuele, nati, Chatuluka kwa Yehova chinthu ichi; sitingathe kunena ndi iwe choipa kapena chabwino.


Taonani, Yehova anaima pamwamba pake, nati, Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu atate wako, ndi Mulungu wa Isaki; dziko limene ulinkugonamo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako;


Ndipo Mulungu anadza kwa Labani Mwaramu usiku, nati kwa iye, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.


Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isaki zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandichotsa ine wopanda kanthu m'manja. Mulungu anakuona kusauka kwanga, ndi ntchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero.


ndipo anati kwa iwo, Ndiona ine nkhope ya atate wanu kuti siindionekere ine monga kale; koma Mulungu wa atate wanga anali ndi ine.


Mulungu wa Abrahamu ndi Mulungu wa Nahori, Mulungu wa atate wao aweruze pa ife. Ndipo Yakobo analumbirira pa Kuopsa kwa atate wake Isaki.


Ndipo atate wanu wandinyenga ine, nasinthanitsa malipiro anga kakhumi; koma Mulungu sanamlole iye andichitire ine choipa.


Ndipo Abisalomu sanalankhule ndi Aminoni chabwino kapena choipa, pakuti Abisalomu anamuda Aminoni popeza adachepetsa mlongo wake Tamara.


Muzitero naye Hezekiya mfumu ya Yuda, kuti, Asakunyenge Mulungu wako amene umkhulupirira, ndi kuti, Yerusalemu sudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya Asiriya.


Udzitamandiranji ndi choipa, chiphona iwe? Chifundo cha Mulungu chikhala tsiku lonse.


Mfumu inamyankha Daniele, niti, Zoona Mulungu wako ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa mafumu, ndi wovumbulutsa zinsinsi; popeza wakhoza kuvumbulutsa chinsinsi ichi.


Nebukadinezara ananena, nati, Alemekezedwe Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, amene anatuma mthenga wake, napulumutsa atumiki ake omkhulupirira Iye, nasanduliza mau a ine mfumu, napereka matupi ao kuti asatumikire kapena kulambira mulungu wina yense, koma Mulungu waowao.


Ndipo poyandikira padzenje inafuula ndi mau achisoni mfumu, ninena, niti kwa Daniele, Daniele, mnyamata wa Mulungu wamoyo, kodi Mulungu wako, amene umtumikira kosalekeza, wakhoza kukulanditsa kwa mikango?


Ndilamulira ine kuti m'maiko onse a ufumu wanga anthu anjenjemere, naope pamaso pa Mulungu wa Daniele; pakuti Iye ndiye Mulungu wamoyo wakukhala chikhalire, ndi ufumu wake ngwosaonongeka, ndi kulamulira kwake kudzakhala mpaka chimaliziro.


Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pao! Kutacha m'mawa achichita, popeza chikhozeka m'manja mwao.


Koma anati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa