Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 31:18 - Buku Lopatulika

18 ndipo ananka nazo zoweta zake zonse, ndi chuma chake chonse anachisonkhanitsa, zoweta zake anaziona mu Padanaramu, kuti anke kwa Isaki atate wake ku dziko la Kanani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 ndipo ananka nazo zoweta zake zonse, ndi chuma chake chonse anachisonkhanitsa, zoweta zake anaziona m'Padanaramu, kuti anke kwa Isaki atate wake ku dziko la Kanani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Ndipo zoŵeta zonse adazitsogoza namazikusa, pamodzi ndi zonse zimene adazipeza ku Mesopotamiya kuja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 anakusa ziweto zake zonse patsogolo natenga katundu wake yense amene anamupeza ku Padanaramu, ndipo ananyamuka kupita ku Kanaani, ku dziko la abambo ake, Isake.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 31:18
8 Mawu Ofanana  

ndipo Isaki anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Mwaramu wa ku Padanaramu, mlongo wake wa Labani Mwaramu.


Ndipo Esau anamuda Yakobo chifukwa cha mdalitso umene atate wake anamdalitsa nao: ndipo Esau anati m'mtima mwake, Masiku a maliro a atate wanga ayandikira; pamenepo ndipo ndidzamupha mphwanga Yakobo.


kuti ndibwerenso kunyumba ya atate wanga ndi mtendere, pamenepo Yehova adzakhala Mulungu wanga,


Ndipo anauka Yakobo nakweza ana ake ndi akazi ake pa ngamira;


Ndipo amithenga anabwera kwa Yakobo kuti, Tidafika kwa mbale wanu Esau, ndipo iyenso alinkudza kukomana nanu, ndipo ali nao anthu mazana anai.


mphindi yakufunafuna ndi mphindi yakumwazika; mphindi yakusunga ndi mphindi yakutaya;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa