Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 31:15 - Buku Lopatulika

15 Kodi satiyesa ife alendo? Chifukwa anatigulitsa ife, nathanso kuononga ndalama zathu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Kodi satiyesa ife alendo? Chifukwa anatigulitsa ife, nathanso kuononga ndalama zathu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Ife bambo wathu akutiyesa alendo. Adatigulitsa, ndipo ndalama zomwe adazipezera pa ifezo, adamwaza zonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Kodi abambo athu samationa ife ngati alendo? Iwo anatigulitsa ndi kuwononga ndalama zonse anazipeza pa ifezo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 31:15
9 Mawu Ofanana  

Ndipo panali madzulo Labani anatenga Leya mwana wake wamkazi, nadza naye kwa Yakobo, ndipo iye analowa kwa mkaziyo.


Undipatse ine akazi anga ndi ana anga chifukwa cha iwowa ndakutumikira iwe, ndimuke: chifukwa udziwa iwe ntchito imene ndinakugwirira iwe.


Ndipo Rakele ndi Leya anayankha, nati kwa iye, Kodi tili nalonso gawo kapena cholowa m'nyumba ya atate wathu?


Chifukwa kuti chuma chonse Mulungu anachichotsa kwa atate wathu ndi chathu ndi cha ana athu; tsono, zonse wakunenera iwe Mulungu, uchite.


Ndinakhala chotere zaka makumi awiri m'nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe chifukwa cha ana ako aakazi awiri, ndi zaka zisanu ndi chimodzi chifukwa cha zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi.


Ndipo ndinanena nao, Ife monga umo tinakhoza, tinaombola abale athu Ayuda ogulitsidwa kwa amitundu; ndipo kodi inu mukuti mugulitse abale anu, kapena tiwagule ndi ife? Pamenepo anakhala duu, nasowa ponena.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa