Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 31:13 - Buku Lopatulika

13 Ine ndine Mulungu wa ku Betele, kuja unathira mafuta pamwala paja, pamene unandilumbirira ine chilumbiriro: tsopano uka, nuchoke m'dziko lino, nubwerere ku dziko la abale ako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ine ndine Mulungu wa ku Betele, kuja unathira mafuta pamwala paja, pamene unandilumbirira ine chilumbiriro: tsopano uka, nuchoke m'dziko lino, nubwerere ku dziko la abale ako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Ine ndine Mulungu amene ndidakuwonekera ku Betele kuja kumene udaimika mwala wachikumbutso ndi kuudzoza mafuta, ndipo kumeneko iwe udalumbira. Konzeka tsopano, uchoke kuno, ubwerere ku dziko lakwanu.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ine ndine Mulungu amene ndinadza kwa iwe pa Beteli paja. Beteli ndi kumalo kuja kumene unayimika mwala ndi kuwudzoza mafuta, komanso kulumbira kwa Ine. Tsopano choka mʼdziko lino msanga ndi kubwerera ku dziko la kwanu.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 31:13
7 Mawu Ofanana  

Mthenga wa Mulungu ndipo anati kwa ine m'kulotamo, Yakobo; nati ine, Ndine pano.


Ndipo Rakele ndi Leya anayankha, nati kwa iye, Kodi tili nalonso gawo kapena cholowa m'nyumba ya atate wathu?


Ndipo Yehova anati kwa Yakobo, Bwera ku dziko la atate wako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakhala ndi iwe.


Ndipo Yakobo anati, Mulungu wa atate wanga Abrahamu, Mulungu wa atate wanga Isaki, Yehova, amene munati kwa ine, Bwera ku dziko lako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakuchitira iwe bwino:


Ndipo Mulungu anati kwa Yakobo, Nyamuka nukwere kunka ku Betele nukhale kumeneko: numange kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anaonekera kwa iwe pamene unathawa ku nkhope ya Esau mbale wako.


Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, natcha pamenepo El Betele: pakuti kumeneko Mulungu anaonekera kwa iye muja anathawa pa nkhope ya mbale wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa