Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 30:38 - Buku Lopatulika

38 Ndipo anaimitsa nthyole zimene anazikupula pandunji ndi zoweta m'michera yakumwera, m'mene ziweto zinafika kumweramo ndipo zidatenga mabere pamene zinadza kumwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

38 Ndipo anaimitsa nthyole zimene anazikupula pandunji ndi zoweta m'michera yakumwera, m'mene ziweto zinafika kumweramo ndipo zidatenga mabere pamene zinadza kumwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

38 Nthambizo adaziika patsogolo pa zoŵeta kumene zinkamwera madzi, kuti zoŵetazo ziziyang'ana nthambizo pomwa madzi, chifukwa zoŵetazo zinkakwerewa podzamwa madzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

38 Atatero anayika nthambi zija mʼmagome omwera madzi molunjika ziweto zija kuti pakumwa madziwo ziweto zazikazi ziziyangʼana nthambi zija popeza kuti pakumwa madzi ziweto zija zinkakwerana.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 30:38
3 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anatenga nthyole za mtengo wauwisi wa libne, ndi za mtengo wakatungurume, ndi za mtengo waarimoni, nakupula m'menemo mizere yoyera, naonetsa moyera mwa m'nthyolemo.


Ndipo ziweto zinatenga mabere patsogolo pa nthyolezo, ndipo zoweta zinabala zamipyololomipyololo, ndi mathothomathotho, ndi zamawangamawanga.


Ndipo panali pamene zoweta zolimba zidatenga mabere, Yakobo anaika nthyole pamaso pa zoweta m'micheramo kuti zitenge mabere pa nthyolezo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa