Genesis 30:35 - Buku Lopatulika35 Tsiku lomwelo Labani anachotsa atonde amene anali amipyololomipyololo ndi amathothomathotho, ndi mbuzi zazikazi zinali zamawangamawanga ndi zamathothomathotho zonse zinali zoyera pang'ono, ndi zakuda zonse za nkhosa, napatsa m'dzanja la ana ake aamuna. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201435 Tsiku lomwelo Labani anachotsa atonde amene anali amipyololomipyololo ndi amathothomathotho, ndi mbuzi zazikazi zinali zamawangamawanga ndi zamathothomathotho zonse zinali zoyera pang'ono, ndi zakuda zonse za nkhosa, napatsa m'dzanja la ana ake amuna. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa35 Koma tsiku limenelo, Labani adachotsa atonde onse amathothomathotho ndi amaŵangamaŵanga, kudzanso mbuzi zazikazi zamathothomathotho ndi zamaŵangamaŵanga, zonse za maŵanga oyera. Adachotsanso nkhosa zonse zakuda, nauza ana ake kuti aziyang'anire zoŵeta zonsezo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero35 Tsiku lomwelo Labani anachotsa atonde onse ndi mbuzi zazikazi zonse zimene zinali ndi mawangamawanga kapena zamathothomathotho, ndiponso zonse zabanga loyera. Anachotsa ana onse ankhosa aakazi akuda, napereka ziweto zonsezi kwa ana ake aamuna kuti aziweta. Onani mutuwo |