Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 29:34 - Buku Lopatulika

34 Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna, nati, Tsopano lino mwamuna wanga adzadziphatika kwa ine chifukwa ndambalira iye ana aamuna atatu; chifukwa chake anamutcha dzina lake Levi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna, nati, Tsopano lino mwamuna wanga adzadziphatika kwa ine chifukwa ndambalira iye ana amuna atatu; chifukwa chake anamutcha dzina lake Levi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Adatenganso pena pathupi, nabalanso mwana wina wamwamuna, ndipo adati, “Tsopano mwamuna wanga azindikonda kwambiri, popeza kuti ndamubalira ana aamuna atatu.” Motero mwanayo adamutcha Levi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Anatenganso pathupi kachitatu, ndipo pamene anabereka mwana wamwamuna anati, “Pano pokha tidzaphatikana kwambiri ndi mwamuna wanga, chifukwa ndamubalira ana aamuna atatu.” Kotero anamutcha dzina lake Levi.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 29:34
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Leya anati, Mulungu anandipatsa ine mphatso yabwino; tsopano mwamuna wanga adzakhala ndi ine, chifukwa ndambalira iye ana aamuna asanu ndi mmodzi; ndipo anamutcha dzina lake Zebuloni.


Ndipo panali tsiku lachitatu pamene anamva kuwawa, ana aamuna awiri a Yakobo, Simeoni ndi Levi, abale ake a Dina, anatenga wina lupanga lake wina lake, nalimbika mtima nalowa m'mzinda napha amuna onse.


ana aamuna a Leya: ndiwo Rubeni mwana woyamba wa Yakobo, ndi Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Zebuloni, ndi Isakara;


Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.


Ndi ana aamuna a Levi: Geresoni, Kohati, ndi Merari.


Ndipo anamuka munthu wa banja la Levi, natenga mwana wamkazi wa Levi.


Mwa fuko la Simeoni zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko Levi zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Isakara zikwi khumi ndi ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa