Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 29:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo Yakobo anati kwa Labani, Undipatse ine mkazi wanga, chifukwa masiku anga atha, kuti ndilowe kwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo Yakobo anati kwa Labani, Undipatse ine mkazi wanga, chifukwa masiku anga atha, kuti ndilowe kwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Yakobe adauza Labani kuti, “Tsopano nthaŵi yatha. Patseni mwana wanuyu kuti ndimkwatire.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Kenaka Yakobo anati kwa Labani, “Nthawi yanga ndakwanitsa, ndipatseni mwana wanu kuti ndimukwatire.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 29:21
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anamkonda Rakele, nati, Ndidzakutumikirani inu zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele mwana wanu wamkazi wamng'ono.


Ndipo Yakobo anamtumikira zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele; koma zidamuonekera iye ngati masiku owerengeka chifukwa cha chikondi chimene anamkonda iye nacho.


Ndipo Labani anasonkhanitsa anthu onse a kumeneko nakonzera madyerero.


Ndinakhala chotere zaka makumi awiri m'nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe chifukwa cha ana ako aakazi awiri, ndi zaka zisanu ndi chimodzi chifukwa cha zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi.


Ndipo iye anapatukira kwa mkazi panjira, nati, Tiyetu, ndilowane nawe; chifukwa sanamdziwe kuti ndiye mpongozi wake. Ndipo anati, Kodi udzandipatsa ine chiyani kuti ulowane ndi ine.


Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.


Ndipo kubadwa kwake kwa Yesu Khristu kunali kotere: Amai wake Maria anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera.


Munthu akatenga mkazi, nalowana naye, namuda,


Ndipo kunali atapita masiku, nyengo ya kucheka tirigu Samisoni anakacheza ndi mkazi wake ndi kumtengera mwanawambuzi, nati, Ndidzalowa kwa mkazi wanga kuchipinda. Koma atate wake sanamlole kulowamo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa