Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 29:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo Yakobo anamtumikira zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele; koma zidamuonekera iye ngati masiku owerengeka chifukwa cha chikondi chimene anamkonda iye nacho.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo Yakobo anamtumikira zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele; koma zidamuonekera iye ngati masiku owerengeka chifukwa cha chikondi chimene anamkonda iye nacho.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Motero Yakobe adagwira ntchito zaka zisanu ndi ziŵiri kuti akwatire Rakele, ndipo nthaŵi imeneyo idangooneka kwa iye ngati masiku oŵerengeka chabe, chifukwa choti adaamkonda kwambiri mkaziyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Choncho Yakobo anagwira ntchito zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele. Koma kwa iye zaka zonsezi zinakhala ngati masiku wochepa chifukwa anamukonda Rakele.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 29:20
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Isaki anamlowetsa mkaziyo m'hema wa amake Sara, namtenga Rebeka, nakhala iye mkazi wake; ndipo anamkonda iye; ndipo Isaki anatonthozedwa mtima atafa amake.


Ndipo anati Labani, Kuli kwabwino kuti ndimpatse iwe osampatsa kwa mwamuna wina; ukhalebe ndi ine.


Umalize sabata lake la uyu, ndipo ndidzakupatsa uyonso chifukwa cha utumiki umene udzanditumikirawo kuonjezera zaka zina zisanu ndi ziwiri.


Ndipo Yakobo analowanso kwa Rakele, namkondanso Rakele kopambana Leya, namtumikira Labani zaka zisanu ndi ziwiri zinanso.


Undipatse ine akazi anga ndi ana anga chifukwa cha iwowa ndakutumikira iwe, ndimuke: chifukwa udziwa iwe ntchito imene ndinakugwirira iwe.


Kodi satiyesa ife alendo? Chifukwa anatigulitsa ife, nathanso kuononga ndalama zathu.


Ndipo mnyamatayo sanachedwe kuchichita popeza anakondwera ndi mwana wake wamkazi wa Yakobo; ndipo iye anali wolemekezedwa woposa onse a pa banja la atate wake.


Ndipo Yakobo anathawira kuthengo la Aramu, ndi Israele anagwira ntchito chifukwa cha mkazi, ndi chifukwa cha mkazi anaweta nkhosa.


Ndipo mwa mneneri Yehova anakweretsa Israele kuchokera mu Ejipito, ndi mwa mneneri anasungika.


chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.


Pakuti chikondi cha Khristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti mmodzi adafera onse, chifukwa chake onse adafa;


ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.


Ndipo anyamata a Saulo analankhula mau awa m'makutu a Davide. Nati Davide, Kodi muchiyesera chinthu chopepuka kukhala mkamwini wa mfumu, popeza ndili munthu wosauka, ndi wopeputsidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa