Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 25:31 - Buku Lopatulika

31 Ndipo Yakobo anati, Tigulane lero ukulu wako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Ndipo Yakobo anati, Tigulane lero ukulu wako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Koma Yakobe adayankha kuti, “Uyambe wandipatsa ukulu wako wauchisamba, ndiye ndikupatse zimenezi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Yakobo anayankha, “Choyamba undigulitse ukulu wako.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 25:31
9 Mawu Ofanana  

ndipo Esau anati kwa Yakobo, Undipatse ndidye chofiiracho; chifukwa ndalefuka: chifukwa chake anamutcha dzina lake Edomu.


Ndipo Esau anati, Taona, ine ndifuna kufa: ukuluwo ndidzapindulanji nao?


Ndipo iye anati, Kodi si ndicho chifukwa anamutcha dzina lake Yakobo? Kuti wandinyenga ine kawiri aka; analanda ukulu wanga ndipo taonani, tsopano walanda mdalitso wanga. Ndipo anati, Kodi simunandisungire ine mdalitso?


Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.


Ndipo ana a Rubeni mwana woyamba wa Israele, (pakuti ndiye mwana woyamba; koma popeza anaipsa kama wa atate wake ukulu wake unapatsidwa kwa ana a Yosefe mwana wa Israele, koma m'buku la chibadwidwe asayesedwe monga mwa ukulu wake.


Pakuti Yuda anakula mphamvu mwa abale ake, ndi mtsogoleri anafuma kwa iyeyu, koma ukulu ngwa Yosefe);


pamenepo kudzali, tsiku lakugawira ana ake aamuna chuma chake, sangakhoze kuyesa mwana wa wokondana naye woyamba kubadwa, wosati mwana wa wodana naye, ndiye woyamba kubadwatu.


Koma azivomereza wobadwa woyamba, mwana wa wodana naye, ndi kumwirikizira gawo lake la zake zonse; popeza iye ndiye chiyambi cha mphamvu yake; zoyenera woyamba kubadwa nzake.


kuti pangakhale wachigololo, kapena wamnyozo, ngati Esau, amene anagulitsa ukulu wake wobadwa nao mtanda umodzi wa chakudya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa