Ezara 9:9 - Buku Lopatulika9 Popeza ife ndife akapolo, koma Mulungu wathu sanatisiye mu ukapolo wathu, natifikitsira chifundo pamaso pa mafumu a Persiya, kuti atitsitsimutse kuimika nyumba ya Mulungu wathu, ndi kukonzanso muunda wake, ndi kutipatsa linga mu Yuda ndi mu Yerusalemu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Popeza ife ndife akapolo, koma Mulungu wathu sanatisiye m'ukapolo wathu, natifikitsira chifundo pamaso pa mafumu a Persiya, kuti atitsitsimutse kuimika nyumba ya Mulungu wathu, ndi kukonzanso muunda wake, ndi kutipatsa linga m'Yuda ndi m'Yerusalemu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Inde ndife akapolo, komabe Inu Mulungu wathu simudatisiya mu ukapolo, mwatiwonetsa chikondi chanu chosasinthika pamaso pa mafumu a ku Persiya. Mwatitsitsimutsa kuti timange Nyumba yanu, Inu Mulungu wathu, pa mabwinja ake akale. Mwatitchinjiriza m'dziko la Yudeya ndiponso mu Yerusalemu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Ndifedi akapolo. Koma Inu Yehova simunatileke mu ukapolo wathu. Mwationetsa chikondi chanu chosasinthika pamaso pa mafumu a ku Perisiya. Mwatitsitsimutsa kuti timange Nyumba yanu pokonzanso mabwinja ake. Mwatitchinjiriza mʼdziko la Yuda ndi Yerusalemu. Onani mutuwo |