Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 9:4 - Buku Lopatulika

4 Nandisonkhanira aliyense wakunjenjemera pa mau a Mulungu wa Israele, chifukwa cha kulakwa kwa iwo a ndende; ndipo ndinakhala m'kudabwa mpaka nsembe yamadzulo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Nandisonkhanira aliyense wakunjenjemera pa mau a Mulungu wa Israele, chifukwa cha kulakwa kwa iwo a ndende; ndipo ndinakhala m'kudabwa mpaka nsembe yamadzulo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ndidakhala pansi choncho kufikira nthaŵi yamadzulo. Tsono anthu onse amene ankaopa mau a Mulungu wa Israele, ataona kusakhulupirika kwa obwerako ku ukapolo aja, adayamba kubwera kwa ine kudzasonkhana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndinakhala pansi chomwecho wokhumudwa mpaka nthawi ya nsembe ya madzulo. Ndipo onse amene ankaopa mawu a Mulungu wa Israeli chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu obwerako ku ukapolo anayamba kubwera kwa ine kudzasonkhana.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 9:4
13 Mawu Ofanana  

popeza mtima wako unali woolowa, ndipo wadzichepetsa pamaso pa Mulungu, pakumva mau ake otsutsana nao malo ano, ndi okhala m'mwemo, ndi kudzichepetsa pamaso panga, ndi kung'amba zovala zako, ndi kulira pamaso panga; Inenso ndakumvera, ati Yehova.


Ndipo tsono tipangane ndi Mulungu wathu kuchotsa akazi onse, ndi obadwa mwa iwo, monga mwa uphungu wa mbuye wanga, ndi wa iwo akunjenjemera pa lamulo la Mulungu wathu; ndipo chichitike monga mwa chilamulo.


Ndipo anasonkhana ku Yerusalemu amuna onse a Yuda ndi Benjamini asanapite masiku atatu, ndiwo mwezi wachisanu ndi chinai, tsiku la makumi awiri a mwezi; nakhala pansi anthu onse m'khwalala pakhomo pa nyumba ya Mulungu, alikunjenjemera chifukwa cha mlandu uwu, ndi chifukwa cha mvulayi.


Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi, popeza sasamalira chilamulo chanu.


Mwanawankhosa wina ukonze m'mawa; ndi mwanawankhosa wina ukonze madzulo;


Ndi mwanawankhosa wina ukonze madzulo; umkonze umo unachitira nsembe yaufa cha m'mawa ndi nsembe yake yothira, akhale fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.


Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.


Imvani mau a Yehova, inu amene munthunthumira ndi mau ake; abale anu amene akudani inu, amene anaponya inu kunja chifukwa cha dzina langa, iwo anati, Yehova alemekezedwe, kuti ife tione kusangalala kwanu; koma iwo adzakhala ndi manyazi.


Ndipo Yehova ananena naye, Pita pakati pa mzinda, pakati pa Yerusalemu, nulembe chizindikiro pa mphumi zao za anthu akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa pakati pake.


Masiku aja ine Daniele ndinali kulira masabata atatu amphumphu.


inde pakunena ine m'kupemphera, munthu uja Gabriele, amene ndidamuona m'masomphenya poyamba paja, anauluka mwaliwiro nandikhudza ngati nthawi yakupereka nsembe ya madzulo.


Ndipo, taonani, anadza wina wa ana a Israele, nabwera naye mkazi Mmidiyani kudza naye kwa abale ake, pamaso pa Mose, ndi pamaso pa khamu lonse la ana a Israele, pakulira iwo pa khomo la chihema chokomanako.


Koma Petro ndi Yohane analikukwera kunka ku Kachisi pa ora lakupembedza, ndilo lachisanu ndi chinai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa