Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 9:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo pakumva mau awa ndinang'amba chovala changa, ndi malaya anga, ndi kumwetula tsitsi la pamutu panga ndi ndevu zanga, ndi kukhala pansi m'kudabwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo pakumva mau awa ndinang'amba chovala changa, ndi malaya anga, ndi kumwetula tsitsi la pamutu panga ndi ndevu zanga, ndi kukhala pansi m'kudabwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Nditamva zimenezi, ndidang'amba zovala zanga ndi mwinjiro wanga chifukwa cha chisoni, ndipo ndidazula tsitsi la kumutu kwanga ndi kumwetsula ndevu zanga, nkukhala pansi ndili wotaya mtima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Nditamva zimenezi, ndinangʼamba chovala changa ndi mwinjiro wanga ndipo ndinamwetula tsitsi la kumutu kwanga ndi ndevu zanga nʼkukhala pansi ndili wokhumudwa.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 9:3
21 Mawu Ofanana  

Pomwepo Davide anagwira zovala zake nazing'amba; nateronso anthu onse okhala naye.


Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba, ndi Sebina mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolembera mbiri, anadza kwa Hezekiya ndi zovala zao zong'ambika, namuuza mau a kazembeyo.


Ndipo kunali, pakumva mau awa, ndinakhala pansi ndi kulira misozi, ndi kuchita maliro masiku ena, ndinasalanso, ndi kupemphera pamaso pa Mulungu wa Kumwamba,


Ndipo ndinatsutsana nao, ndi kuwatemberera, ndi kukantha ena a iwo, ndi kumwetula tsitsi lao, ndi kuwalumbiritsa pa Mulungu ndi kuti, Musapereke ana anu aakazi kwa ana ao aamuna, kapena kutengera ana anu aamuna, kapena a inu nokha, ana ao aakazi.


Pamenepo Yobu ananyamuka, nang'amba malaya ake, nameta mutu wake, nagwa pansi, nalambira,


Ndinasumwa kwakukulu, chifukwa cha oipa akusiya chilamulo chanu.


Potero mzimu wanga wakomoka mwa ine; mtima wanga utenga nkhawa m'kati mwanga.


Nenani kwa Mulungu, Ha, ntchito zanu nzoopsa nanga! Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu.


Akwera ku Kachisi, ndi ku Diboni, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Mowabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndevu zonse zametedwa.


Ndipo sanaope, sanang'ambe nsalu zao, kapena mfumu, kapena atumiki ake aliyense amene anamva mau onsewa.


Meta tsitsi lako, iwe Yerusalemu, nulitaye, nukweze maliro pa mapiri oti see; pakuti Yehova wakana ndi kusiya mbadwo umene aukwiyira.


Ndipo ndinafika kwa andende ku Telabibu, okhala kumtsinje Kebara, ndiko kwao; ndipo ndinakhalako wodabwa pakati pao masiku asanu ndi awiri.


Ndipo adzadzimangira m'chuuno ndi ziguduli, ndi zoopsetsa zidzawaphimba, ndi nkhope zonse zidzachita manyazi, ndi mitu yao yonse idzachita dazi.


Pamenepo Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara anadabwa nthawi, namsautsa maganizo ake. Mfumu inayankha, niti, Belitesazara, lisakusautse lotoli, kapena kumasulira kwake. Belitesazara anayankha, nati, Mbuye wanga, lotoli likadakhala la iwo akudana nanu, ndi kumasulira kwake kwa iwo akuutsana nanu.


Ndipo ine Daniele ndinakomoka ndi kudwala masiku ena; pamenepo ndinauka ndi kuchita ntchito ya mfumu; ndipo ndinadabwa nao masomphenyawo, koma panalibe wakuwazindikiritsa.


Asamete tsitsi la pamutu pao, kapena kuchecherera ndevu zao, kapena kudzicheka matupi ao.


Udziyeseze wadazi, udzimete wekha chifukwa cha ana ako okondwera nao; kuza dazi lako ngati la muimba; pakuti anakuchokera, nalowa ndende.


Ndipo Yoswa anang'amba zovala zake, nagwa nkhope yake pansi, ku likasa la Yehova, mpaka madzulo, iye ndi akuluakulu a Israele, nathira fumbi pamitu pao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa