Ezara 8:34 - Buku Lopatulika34 zonsezi anaziwerenga ndi kuziyesa; ndi kulemera kwake konse kunalembedwa nthawi yomweyo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201434 zonsezi anaziwerenga ndi kuziyesa; ndi kulemera kwake konse kunalembedwa nthawi yomweyo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa34 Zonsezo adaziŵerenga ndi kuziyesa ndipo adalemba kulemera kwa chinthu chilichonse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero34 Zonsezi anaziwerenga ndi kuziyeza ndipo analemba kulemera kwa chinthu chilichonse. Onani mutuwo |
Otengedwa ndende, atatuluka m'ndende, anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israele, ng'ombe khumi ndi ziwiri za Aisraele onse, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi imodzi, anaankhosa makumi asanu ndi awiri mphambu asanu ndi awiri, atonde khumi ndi awiri, akhale nsembe yazolakwa; zonsezi ndizo nsembe yopsereza ya kwa Yehova.