Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 8:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo akulu a nyumba za makolo ndi awa, ndi chibadwidwe cha iwo okwera nane limodzi kuchokera ku Babiloni, pokhala mfumu Arita-kisereksesi, ndi ichi:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo akulu a nyumba za makolo ndi awa, ndi chibadwidwe cha iwo okwera nane limodzi kuchokera ku Babiloni, pokhala mfumu Arita-kisereksesi, ndi ichi:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Nawu mndandanda wa maina a atsogoleri a mabanja amene adabwera nane kuchokera ku Babiloni, pa nthaŵi ya ufumu wa Arita-kisereksesi:

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Nawa mayina a atsogoleri a mabanja amene anabwera nane kuchokera ku Babuloni nthawi ya ulamuliro wa mfumu Aritasasita:

Onani mutuwo Koperani




Ezara 8:1
16 Mawu Ofanana  

Awanso anachita maere monga abale ao ana a Aroni, pamaso pa Davide mfumu, ndi Zadoki, ndi Ahimeleki, ndi akulu a nyumba za makolo za ansembe ndi Alevi; mkulu wa nyumba za makolo monga mng'ono wake.


Ndi abale ake ngwazi ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri, akulu a nyumba za makolo, amene mfumu Davide anaika akhale oyang'anira a Arubeni, ndi Agadi, ndi hafu la fuko la Manase, pa zinthu zonse za Mulungu ndi zinthu za mfumu.


ndi midzi yao yonse pozungulira pake pa mizinda yomweyi, mpaka Baala. Apo ndi pokhala pao ndipo ali nao mawerengedwe a maina ao.


Ndipo Aisraele onse anawerengedwa mwa chibadwidwe chao; ndipo taonani, alembedwa m'buku la mafumu a Israele; ndipo Yuda anatengedwa ndende kunka ku Babiloni chifukwa cha kulakwa kwao.


Awa ndi akulu a nyumba za makolo a Alevi mwa mibadwo yao, ndiwo akulu; anakhala ku Yerusalemu awa.


Chiwerengo chonse cha akulu a nyumba za makolo, ndiwo ngwazi zamphamvu, ndicho zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi.


Pamenepo ananyamuka akulu a nyumba za makolo a Yuda ndi Benjamini, ndi ansembe, ndi Alevi, ndiwo onse amene Mulungu adawautsira mzimu wao akwere kukamanga nyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu.


ndiwo amene adadza ndi Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Seraya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu, Baana. Kuwerenga kwa amuna a anthu a Israele ndiko:


ana a Parosi, zikwi ziwiri ndi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.


Awa anafunafuna maina ao m'buku la iwo owerengedwa mwa chibadwidwe chao, koma osawapeza; potero anachotsedwa ku ntchito ya nsembe monga odetsedwa.


Ndilamulira kuti onse a ana a Israele, ndi ansembe ao, ndi Alevi, mu ufumu wanga, ofuna eni ake kumuka ku Yerusalemu, apite nawe.


nandifikitsira chifundo pamaso pa mfumu, ndi aphungu ake, ndi pamaso pa akalonga amphamvu onse a mfumu. Motero ndinalimbika mtima, monga umo dzanja la Yehova Mulungu wanga linakhala pa ine; ndipo ndinasonkhanitsa mwa Israele anthu omveka akwere nane limodzi.


Ezara amene anakwera kuchokera ku Babiloni, ndiye mlembi waluntha m'chilamulo cha Mose, chimene Yehova Mulungu wa Israele adachipereka; ndipo mfumu inampatsa chopempha iye chonse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wake.


Nakweranso kunka ku Yerusalemu ena a ana a Israele, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi oimbira, ndi odikira, ndi antchito a m'kachisi, chaka chachisanu ndi chiwiri cha Arita-kisereksesi mfumu.


wa ana a Finehasi, Geresomo; wa ana a Itamara, Daniele; wa ana a Davide, Hatusi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa