Ezara 7:9 - Buku Lopatulika9 Pakuti tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndilo chiyambi cha ulendo wokwera kuchokera ku Babiloni, ndi tsiku loyamba la mwezi wachisanu anafika ku Yerusalemu, monga linamkhalira dzanja lokoma la Mulungu wake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Pakuti tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndilo chiyambi cha ulendo wokwera kuchokera ku Babiloni, ndi tsiku lachimodzi la mwezi wachisanu anafika ku Yerusalemu, monga linamkhalira dzanja lokoma la Mulungu wake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Adanyamuka ku Babiloni pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu, nafika ku Yerusalemu ndi chithandizo cha Mulungu wake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Iye anayamba ulendo wochoka ku Babuloni pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndipo anafika ku Yerusalemu pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu chifukwa dzanja labwino la Mulungu wake linali pa iye. Onani mutuwo |