Ezara 7:6 - Buku Lopatulika6 Ezara amene anakwera kuchokera ku Babiloni, ndiye mlembi waluntha m'chilamulo cha Mose, chimene Yehova Mulungu wa Israele adachipereka; ndipo mfumu inampatsa chopempha iye chonse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ezara amene anakwera kuchokera ku Babiloni, ndiye mlembi waluntha m'chilamulo cha Mose, chimene Yehova Mulungu wa Israele adachipereka; ndipo mfumu inampatsa chopempha iye chonse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Ezarayu anali wophunzira kwambiri wa za Malamulo amene Chauta, Mulungu wa Israele, adaapereka kwa Mose. Popeza kuti Chauta, Mulungu wake, adaamdalitsa Ezarayo, mfumu Arita-kisereksesi ankamupatsa zonse zimene ankapempha. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Ezara ameneyu anabwera kuchokera ku Babuloni. Iyeyu anali wophunzira kwambiri za malamulo a Mose, amene Yehova Mulungu wa Israeli anapereka. Mfumu inamupatsa chilichonse chimene anapempha pakuti dzanja la Yehova Mulungu wake linali pa iye. Onani mutuwo |
Ndipo Ezara mlembi anaima pa chiunda cha mitengo adachimangira msonkhanowo; ndi pambali pake padaima Matitiya, ndi Sema, ndi Anaya, ndi Uriya, ndi Hilikiya, ndi Maaseiya, kudzanja lamanja lake; ndi kudzanja lamanzere Pedaya, ndi Misaele, ndi Malikiya, ndi Hasumu, ndi Hasibadana, Zekariya, ndi Mesulamu.
Chifukwa chanji ndinafika osapeza munthu? Ndi kuitana koma panalibe wina woyankha? Kodi dzanja langa lafupika konse, kuti silingathe kuombola? Pena Ine kodi ndilibe mphamvu zakupulumutsa? Taona pa kudzudzula kwanga ndiumitsa nyanja, ndi kusandutsa mitsinje chipululu; nsomba zake zinunkha chifukwa mulibe madzi, ndipo zifa ndi ludzu.