Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 7:14 - Buku Lopatulika

14 Popeza utumidwa wochokera pamaso pa mfumu ndi aphungu ake asanu ndi awiri, kufunsira za Yuda ndi Yerusalemu monga mwa lamulo la Mulungu wako lili m'dzanja lako,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Popeza utumidwa wochokera pamaso pa mfumu ndi aphungu ake asanu ndi awiri, kufunsira za Yuda ndi Yerusalemu monga mwa lamulo la Mulungu wako lili m'dzanja lako,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Pakuti ine mfumu pamodzi ndi aphungu anga asanu ndi aŵiri tikukutuma kuti ukafunsitse za dziko la Yuda ndi mzinda wa Yerusalemu, kuti ukaone m'mene anthu akutsatira malamulo amene Mulungu wako adaŵapereka kwa iwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Ine mfumu pamodzi ndi alangizi anga asanu ndi awiri tikukutumani kuti mukafufuze za dziko la Yuda ndi mzinda wa Yerusalemu kuti mukaone mmene anthu akutsatira malamulo a Mulungu wanu, amene anawapereka kwa inu.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 7:14
15 Mawu Ofanana  

Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Mulungu wake akhale naye, akwere kunka ku Yerusalemu, ndiwo mu Yuda, nakaimange nyumba ya Yehova Mulungu wa Israele; Iye ndiye Mulungu wokhala mu Yerusalemu.


Adziwe mfumu kuti ife tinamuka kudziko la Yuda, kunyumba ya Mulungu wamkulu, yomangidwa ndi miyala yaikulu, ndi kuikidwa mitengo pamakoma, ndipo inachitika mofulumira ntchitoyi, ndipo inayenda bwino m'dzanja mwao.


ndipo Mulungu wokhalitsa dzina lake komweko agwetse mafumu onse ndi mitundu yonse ya anthu, akutulutsa dzanja lao kusintha mau awa, kuononga nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu. Ine Dariusi ndalamulira, chichitike msanga.


Ndilamuliranso za ichi muzichitira akulu awa a Ayuda, kuti amange nyumba iyi ya Mulungu, ndiko kuti mutengeko chuma cha mfumu, ndicho msonkho wa tsidya la mtsinje, nimupereke zolipira kwa anthu awa msanga, angawachedwetse.


ndi kumuka nazo siliva ndi golide, zimene mfumu ndi aphungu ake, anapereka mwaufulu kwa Mulungu wa Israele, mokhala mwake muli mu Yerusalemu,


nandifikitsira chifundo pamaso pa mfumu, ndi aphungu ake, ndi pamaso pa akalonga amphamvu onse a mfumu. Motero ndinalimbika mtima, monga umo dzanja la Yehova Mulungu wanga linakhala pa ine; ndipo ndinasonkhanitsa mwa Israele anthu omveka akwere nane limodzi.


ndi kuwayesera siliva, ndi golide, ndi zipangizo, ndizo chopereka cha kwa nyumba ya Mulungu wathu, chimene mfumu, ndi aphungu ake, ndi akalonga ake, ndi Aisraele onse anali apawa, adapereka.


a pafupi naye ndiwo Karisena, Setara, Adimata, Tarisisi, Meresi, Marisena, ndi Memukana, akalonga asanu ndi awiri a Persiya ndi Mediya, openya nkhope ya mfumu ndi kukhala oyamba mu ufumu.


Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.


Mfumu inamyankha Daniele, niti, Zoona Mulungu wako ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa mafumu, ndi wovumbulutsa zinsinsi; popeza wakhoza kuvumbulutsa chinsinsi ichi.


Ndipo poyandikira padzenje inafuula ndi mau achisoni mfumu, ninena, niti kwa Daniele, Daniele, mnyamata wa Mulungu wamoyo, kodi Mulungu wako, amene umtumikira kosalekeza, wakhoza kukulanditsa kwa mikango?


Ndilamulira ine kuti m'maiko onse a ufumu wanga anthu anjenjemere, naope pamaso pa Mulungu wa Daniele; pakuti Iye ndiye Mulungu wamoyo wakukhala chikhalire, ndi ufumu wake ngwosaonongeka, ndi kulamulira kwake kudzakhala mpaka chimaliziro.


Tenga a iwo a kundende, a Helidai, a Tobiya, ndi a Yedaya; nudze tsiku lomwelo, nulowe kunyumba ya Yosiya, mwana wa Zefaniya, kumene anafikirako kuchokera ku Babiloni,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa