Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 7:13 - Buku Lopatulika

13 Ndilamulira kuti onse a ana a Israele, ndi ansembe ao, ndi Alevi, mu ufumu wanga, ofuna eni ake kumuka ku Yerusalemu, apite nawe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndilamulira kuti onse a ana a Israele, ndi ansembe ao, ndi Alevi, m'ufumu wanga, ofuna eni ake kumuka ku Yerusalemu, apite nawe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Tsopano ndikupanga lamulo lakuti Mwisraele aliyense kapena ansembe ao, kapena Alevi okhala m'dziko mwanga, amene afuna kuti apite ku Yerusalemu mwaufulu, apite nawe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Tsopano ndikulamula kuti Mwisraeli aliyense, wansembe kapena Mlevi wokhala mʼdziko langa, amene akufuna kupita ku Yerusalemu ndi iwe, apite.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 7:13
11 Mawu Ofanana  

Motero anakhazikitsa mau kulalikira mwa Israele lonse, kuyambira Beereseba kufikira ku Dani, kuti abwere kuchitira Yehova Mulungu wa Israele Paska ku Yerusalemu; pakuti nthawi yaikulu sanachite monga mudalembedwa.


Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Mulungu wake akhale naye, akwere kunka ku Yerusalemu, ndiwo mu Yuda, nakaimange nyumba ya Yehova Mulungu wa Israele; Iye ndiye Mulungu wokhala mu Yerusalemu.


Koma chaka choyamba cha Kirusi mfumu ya Babiloni, Kirusi mfumuyo analamulira kuti azimanga nyumba iyi ya Mulungu.


Pamenepo analamulira Dariusi mfumu, ndipo anthu anafunafuna m'nyumba ya mabuku mosungira chuma mu Babiloni.


Amtokoma anatuluka ofulumizidwa ndi mau a mfumu, ndi lamulo linabukitsidwa m'chinyumba cha ku Susa; ndipo mfumu ndi Hamani anakhala pansi kumwa; koma mzinda wa Susa unadodoma.


Ndipo mfumu inati azichita motero, nalamulira mu Susa, napachikidwa ana aamuna khumi a Hamani.


Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: M'moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha, muli nao mame a ubwana wanu.


Anazikhazikanso kunthawi za nthawi; anazipatsa chilamulo chosatumphika.


Ndilamulira ine kuti m'maiko onse a ufumu wanga anthu anjenjemere, naope pamaso pa Mulungu wa Daniele; pakuti Iye ndiye Mulungu wamoyo wakukhala chikhalire, ndi ufumu wake ngwosaonongeka, ndi kulamulira kwake kudzakhala mpaka chimaliziro.


pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.


Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa