Ezara 6:5 - Buku Lopatulika5 Ndi zipangizo za golide ndi siliva za nyumba ya Mulungu, zimene anazitulutsa Nebukadinezara mu Kachisi ali ku Yerusalemu, nazitenga kunka nazo ku Babiloni, azibwezere, nabwere nazo ku Kachisi ali ku Yerusalemu, chilichonse ku malo ake; naziike m'nyumba ya Mulungu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndi zipangizo za golide ndi siliva za nyumba ya Mulungu, zimene anazitulutsa Nebukadinezara m'Kachisi ali ku Yerusalemu, nazitenga kunka nazo ku Babiloni, azibwezere, nabwere nazo ku Kachisi ali ku Yerusalemu, chilichonse ku malo ake; naziike m'nyumba ya Mulungu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Tsono ziŵiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara adaazitulutsa ku Yerusalemu kunka nazo ku Babiloni, zonsezo zibwezedwe, zipite ku Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Chilichonse chikabwezedwe pamalo pake m'Nyumba ya Mulunguyo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Ndipo ziwiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara anatenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu kupita nazo ku Babuloni, zonsezi zibwezedwe ndipo zipite ku Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Chilichonse chikabwezedwe pamalo pake mʼNyumbayo. Onani mutuwo |
Ndiponso zipangizo za golide ndi siliva za nyumba ya Mulungu, anazitulutsa Nebukadinezara mu Kachisi anali ku Yerusalemu, ndi kubwera nazo ku Kachisi wa ku Babiloni, izizo Kirusi mfumu anazitulutsa mu Kachisi wa ku Babiloni, nazipereka kwa munthu dzina lake Sezibazara, amene anamuika akhale kazembe;