Ezara 6:3 - Buku Lopatulika3 Chaka choyamba cha Kirusi mfumu, analamulira Kirusi mfumuyo, Kunena za nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, imangidwe nyumbayi pamalo pophera nsembe, namangidwe kolimba maziko ake, msinkhu wake mikono makumi asanu ndi limodzi, kupingasa kwake mikono makumi asanu ndi limodzi; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Chaka choyamba cha Kirusi mfumu, analamulira Kirusi mfumuyo, Kunena za nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, imangidwe nyumbayi pamalo pophera nsembe, namangidwe kolimba maziko ake, msinkhu wake mikono makumi asanu ndi limodzi, kupingasa kwake mikono makumi asanu ndi limodzi; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 “Pa chaka choyamba cha ufumu wake, mfumu Kirusi adapereka lamulo lalikulu lonena za Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Adalamula kuti Nyumbayo imangidwenso, ngati malo otsirirako nsembe. Maziko ake ayalidwe mwamphamvu pomwe paja pali maziko ake akale. Muutali mwake idzakhale mamita 27, muufupi mwake idzakhalenso mamita 27. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Mʼchaka choyamba cha ufumu wa Koresi, mfumuyo inapereka lamulo lokhudza Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu. Analamula kuti Nyumba ya Mulungu imangidwenso kukhala malo woperekerako nsembe. Maziko ake amangidwe kolimba pa malo pomwe paja pali maziko ake akale ndipo mulitali mwake mukhale mamita 27, mulifupi mwake mukhale mamita 27. Onani mutuwo |