Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 6:1 - Buku Lopatulika

1 Pamenepo analamulira Dariusi mfumu, ndipo anthu anafunafuna m'nyumba ya mabuku mosungira chuma mu Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Pamenepo analamulira Dariusi mfumu, ndipo anthu anafunafuna m'nyumba ya mabuku mosungira chuma m'Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Atalandira mauwo mfumu Dariusi adapanga lamulo ndipo kafukufuku adachitikadi ku Babiloni m'nyumba mosungira chuma ndi mabuku okhudza mbiri zakale.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Atalandira mawuwo mfumu Dariyo anapereka lamulo ndipo kafukufuku anachitikadi ku Babuloni mʼnyumba yosungira chuma ndi mabuku ambiri yakale.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 6:1
16 Mawu Ofanana  

kuti afunefune m'buku la chikumbutso la makolo anu; momwemo mudzapeza m'buku la chikumbutso, ndi kudziwa kuti mzinda uwu ndi mzinda wopanduka, ndi wosowetsa mafumu, ndi maiko; ndi kuti amadziyendera m'menemo kuyambira kale lomwe; ndicho chifukwa chakuti anapasula mzinda uwu.


Ndipo ndinalamulira anthu, nafunafuna, napeza kuti mzinda uwu unaukira mafumu kuyambira kale lomwe, ndi kuti akachitamo mpanduko ndi kudziyendera.


Ndipo tsono chikakomera mfumu, munthu asanthule m'nyumba ya chuma cha mfumu ili komwe ku Babiloni, ngati nkuterodi, kuti Kirusi mfumu analamulira kuti azimanga nyumba iyi ya Mulungu ku Yerusalemu; ndipo mfumu ititumizire mau omkomera pa chinthuchi.


nasunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi chimwemwe; pakuti Yehova adawakondweretsa, nawatembenuzira mtima wa mfumu ya Asiriya, kulimbitsa manja ao mu ntchito ya nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israele.


Ndilamulira kuti onse a ana a Israele, ndi ansembe ao, ndi Alevi, mu ufumu wanga, ofuna eni ake kumuka ku Yerusalemu, apite nawe.


Ndinali atate wa waumphawi; ndi mlandu wa iye amene sindinamdziwe ndinafunsitsa.


Pamenepo ndinati, Taonani, ndadza; m'buku mwalembedwa za Ine,


Kubisa kanthu ndi ulemerero wa Mulungu; koma ulemerero wa mafumu ndi kusanthula kanthu.


Ndipo za Yehoyakimu mfumu ya Yuda uziti, Yehova atero: Iwe watentha mpukutu uwu, ndi kuti, Bwanji walemba m'menemo, kuti, Mfumu ya ku Babiloni idzadzadi nidzaononga dziko ili, nidzatha m'menemo anthu ndi nyama?


Ndipo Yeremiya anatenga mpukutu wina, naupereka kwa Baruki mlembi, mwana wa Neriya; amene analemba m'menemo ponena Yeremiya mau onse a m'buku lija Yehoyakimu mfumu ya Yuda analitentha m'moto; ndipo anaonjezapo mau ambiri oterewa.


Ndipo pakupenya ine ndinaona dzanja londitulutsira, ndipo taonani, mpukutu wa buku m'mwemo;


Ndipo ananena nane, Wobadwa ndi munthu iwe, Idya chimene wachipeza; idya mpukutu uwu, numuke ndi kunena ndi nyumba ya Israele.


Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi tchemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mavuto.


Ndipo ndinaona m'dzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu buku lolembedwa m'kati ndi kunja kwake, losindikizika ndi zizindikiro zisanu ndi ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa