Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 5:6 - Buku Lopatulika

6 Zolembedwa m'kalata amene Tatenai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setari-Bozenai, ndi anzake Afarisikai, okhala tsidya lino la mtsinje, anatumiza kwa Dariusi mfumu,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Zolembedwa m'kalata amene Tatenai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setari-Bozenai, ndi anzake Afarisikai, okhala tsidya lino la mtsinje, anatumiza kwa Dariusi mfumu,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Nayi kalata yomwe Tatenai, bwanamkubwa wa dera la Patsidya pa Yufurate, ndiponso Setari-Bozenai ndi anzake, akazembe omwe anali m'chigawo cha Patsidya pa Yufurate, adatumiza kwa mfumu Dariusi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Iyi ndi kalata imene Tatenai bwanamkubwa wa dera la patsidya pa Yufurate, ndiponso Setari-Bozenai ndi anzake, akazembe amene anali mʼchigawo cha patsidya pa Yufurate, anatumiza kwa mfumu Dariyo

Onani mutuwo Koperani




Ezara 5:6
7 Mawu Ofanana  

Zolembedwa m'kalatayo anazitumiza kwa Arita-kisereksesi mfumu: ife akapolo anu, anthu a tsidya lino la mtsinjewo, tikupatsani moni.


Pamenepo atawerenga malemba a kalata ya mfumu Arita-kisereksesi kwa Rehumu, ndi Simisai mlembi, ndi anzao, anafulumira kupita ku Yerusalemu kwa Ayuda, nawaletsa ndi dzanja lamphamvu.


nalembera Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi Simisai mlembi, ndi anzake otsala; Adinai, ndi Afarisatikai, Ataripilai, Afarisai, Aereke, Ababiloni, Asusani, Adehai, Aelamu,


Nthawi yomweyi anawadzera Tatenai kazembe tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setari-Bozenai, ndi anzao, nanena nao motere, Anakulamulirani inu ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?


anatumiza kalata kwa iyeyo m'menemo munalembedwa motere, kwa Dariusi mfumu, mtendere wonse.


Tsono iwe, Tatenai, kazembe wa tsidya lija la mtsinjewo, Setari-Bozenai, ndi anzanu Afarisikai, okhala tsidya lija la mtsinje, muzikhala kutali;


Ndipo napereka malamulo a mfumu kwa akazembe a mfumu, ndi kwa ziwanga, tsidya lino la mtsinjewo; ndipo iwo anathandiza anthu ndi nyumba ya Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa