Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 5:5 - Buku Lopatulika

5 Koma diso la Mulungu wao linali pa akulu a Ayuda, ndipo sanawaletse mpaka mlandu unamdzera Dariusi, nabweza mau a mlanduwo m'kalata.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Koma diso la Mulungu wao linali pa akulu a Ayuda, ndipo sanawaletse mpaka mlandu unamdzera Dariusi, nabweza mau a mlanduwo m'kalata.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Koma Mulungu wao ankaŵasamalira atsogoleri a Ayuda, ndipo choncho anthu aja adaganiza zoti asaŵaletse Ayudawo kumanga mpaka atalembera mfumu Dariusi kalata, nkulandiranso yankho lake pa nkhani imeneyi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Koma Mulungu wawo amayangʼanira atsogoleri Ayuda, motero kuti anthu aja anaganiza kuti asawaletse kumanga Nyumbayo mpaka atalembera mfumu Dariyo kalata ndi kulandira yankho lake.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 5:5
12 Mawu Ofanana  

Pakuti maso a Yehova ayang'ana uko ndi uko m'dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi Iye. Mwachita chopusa m'menemo; pakuti kuyambira tsopano mudzaona nkhondo.


nandifikitsira chifundo pamaso pa mfumu, ndi aphungu ake, ndi pamaso pa akalonga amphamvu onse a mfumu. Motero ndinalimbika mtima, monga umo dzanja la Yehova Mulungu wanga linakhala pa ine; ndipo ndinasonkhanitsa mwa Israele anthu omveka akwere nane limodzi.


Ezara amene anakwera kuchokera ku Babiloni, ndiye mlembi waluntha m'chilamulo cha Mose, chimene Yehova Mulungu wa Israele adachipereka; ndipo mfumu inampatsa chopempha iye chonse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wake.


Pakuti ndinachita manyazi kupempha kwa mfumu gulu la asilikali, ndi apakavalo, kutithandiza pa adani panjira; popeza tidalankhula ndi mfumu kuti, Dzanja la Mulungu wathu likhalira mokoma onse akumfuna; koma mphamvu yake ndi mkwiyo wake zitsutsana nao onse akumsiya.


Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.


Taonani, diso la Yehova lili pa iwo akumuopa Iye, pa iwo akuyembekeza chifundo chake.


Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwao.


Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani; chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.


osaopa adani m'kanthu konse, chimene chili kwa iwowa chisonyezo cha chionongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu;


Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lao; koma nkhope ya Ambuye ili pa ochita zoipa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa