Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ezara 5:3 - Buku Lopatulika

3 Nthawi yomweyi anawadzera Tatenai kazembe tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setari-Bozenai, ndi anzao, nanena nao motere, Anakulamulirani inu ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Nthawi yomweyi anawadzera Tatenai kazembe tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setari-Bozenai, ndi anzao, nanena nao motere, Anakulamulirani inu ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Nthaŵi yomweyo Tatenai, bwanamkubwa wa chigawo cha Patsidya pa Yufurate ndi Setari-Bozenai, pamodzi ndi anzao adapita kwa iwowo, ndipo adalankhula nawo naŵafunsa kuti, “Adakulamulani ndani kuti mumange Nyumba imeneyi ndi kumaliza khoma lake?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Pa nthawi imeneyo Tatenai, bwanamkubwa wa chigawo cha patsidya pa Yufurate pamodzi ndi Setari-Bozenai ndi anzawo anapita kwa iwo ndi kukawafunsa kuti, “Anakulolani ndani kuti mumangenso Nyumba imeneyi ndi kutsiriza khoma lake?”

Onani mutuwo Koperani




Ezara 5:3
12 Mawu Ofanana  

Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Mulungu wake akhale naye, akwere kunka ku Yerusalemu, ndiwo mu Yuda, nakaimange nyumba ya Yehova Mulungu wa Israele; Iye ndiye Mulungu wokhala mu Yerusalemu.


Adziwe mfumu kuti, Ayuda adakwerawo ochokera kwanu atifikira ife ku Yerusalemu, alikumanga mzinda uja wopanduka ndi woipa, alikutsiriza malinga ake, nalumikiza maziko ake.


nalembera Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi Simisai mlembi, ndi anzake otsala; Adinai, ndi Afarisatikai, Ataripilai, Afarisai, Aereke, Ababiloni, Asusani, Adehai, Aelamu,


Zolembedwa m'kalata amene Tatenai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setari-Bozenai, ndi anzake Afarisikai, okhala tsidya lino la mtsinje, anatumiza kwa Dariusi mfumu,


Pamenepo tinafunsa akulu aja ndi kutere nao, Anakulamulirani ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?


Pamenepo Tatenai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, Setari-Bozenai, ndi anzao, popeza mfumu Dariusi adatumiza mau, anachita momwemo chofulumira.


Tsono iwe, Tatenai, kazembe wa tsidya lija la mtsinjewo, Setari-Bozenai, ndi anzanu Afarisikai, okhala tsidya lija la mtsinje, muzikhala kutali;


Ndipo ine Arita-kisereksesi, mfumu ine, ndilamulira osunga chuma onse okhala tsidya lija la mtsinjewo, kuti chilichonse akupemphani Ezara wansembe, mlembi wa lamulo la Mulungu wa Kumwamba, chichitike mofulumira;


Chaka chachiwiri cha mfumu Dariusi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri kwa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kuti,


Ndipo m'mene Iye analowa mu Kachisi, ansembe aakulu ndi akulu a anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?


Ndipo m'mene anawaimika pakati, anafunsa kuti, Ndi mphamvu yanji, kapena m'dzina lanji, mwachita ichi inu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa