Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 5:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo aneneri, Hagai mneneriyo, ndi Zekariya mwana wa Ido, ananenera kwa Ayuda okhala mu Yuda ndi mu Yerusalemu; m'dzina la Mulungu wa Israele ananenera kwa iwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo aneneri, Hagai mneneriyo, ndi Zekariya mwana wa Ido, ananenera kwa Ayuda okhala m'Yuda ndi m'Yerusalemu; m'dzina la Mulungu wa Israele ananenera kwa iwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Nthaŵi imeneyo aneneri aŵa, Hagai ndi Zekariya mwana wa Ido, adayamba kulankhula kwa Ayuda okhala m'dziko la Yuda ndi mu Yerusalemu. Ankalankhula m'dzina la Mulungu wa Israele amene anali nawo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Nthawi imeneyo aneneri Hagai ndi Zekariya, mwana wa Ido, ankayankhula kwa Ayuda okhala mʼdziko la Yuda ndi mu Yerusalemu mʼdzina la Mulungu wa Israeli, amene anali nawo.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 5:1
9 Mawu Ofanana  

Momwemo inalekeka ntchito ya nyumba ya Mulungu yokhala ku Yerusalemu; nilekeka mpaka chaka chachiwiri cha ufumu wa Dariusi mfumu ya Persiya.


Ndipo akulu a Ayuda anamanga opanda chosoweka, mwa kunenera kwa mneneri Hagai, ndi Zekariya mwana wa Ido. Naimanga, naitsiriza, monga mwa lamulo la Mulungu wa Israele, ndi monga mwa lamulo la Kirusi, ndi Dariusi, ndi Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya.


Ndipo adzaimirira, nadzadyetsa nkhosa zake mu mphamvu ya Yehova, mu ukulu wa dzina la Yehova Mulungu wake; ndipo iwo adzakhalabe; pakuti pamenepo Iye adzakhala wamkulu kufikira malekezero a dziko lapansi.


Chaka chachiwiri cha mfumu Dariusi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri kwa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kuti,


Pamenepo mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti,


Musamalire, kuyambira lero ndi m'tsogolo, kuyambira tsiku la makumi awiri ndi chinai la mwezi wachisanu ndi chinai, kuyambira tsiku lija anamanga maziko a Kachisi wa Yehova, samalirani.


Atero Yehova wa makamu: Alimbike manja anu, inu akumva masiku ano mau awa pakamwa pa aneneri amene anakhalako tsiku lakuikidwa maziko a nyumba ya Yehova wa makamu, ndiyo Kachisi, kuti amangidwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa