Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 4:9 - Buku Lopatulika

9 nalembera Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi Simisai mlembi, ndi anzake otsala; Adinai, ndi Afarisatikai, Ataripilai, Afarisai, Aereke, Ababiloni, Asusani, Adehai, Aelamu,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 nalembera Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi Simisai mlembi, ndi anzake otsala; Adinai, ndi Afarisatikai, Ataripilai, Afarisai, Aereke, Ababiloni, Asusani, Adehai, Aelamu,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Kalatayi ikuchokera kwa Rehumu bwanamkubwa, mlembi Simisai ndi anzao aŵa: aweruzi, nduna ndi akuluakulu ena, anthu a ku Persiya ndi ku Ereki, ku Babiloniya, ndi ku Susa, m'dziko la Elami.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Kalata yochokera kwa Rehumu, mkulu wa gulu lankhondo, mlembi Simisai ndi anzawo awa: oweruza, nduna, akuluakulu ena, anthu a ku Peresiya, Ereki, Babuloni, Susa mʼdziko la Elamu,

Onani mutuwo Koperani




Ezara 4:9
16 Mawu Ofanana  

Ana aamuna a Semu; Elamu, ndi Asiriya, ndi Aripakisadi, ndi Ludi, ndi Aramu.


Ndipo mfumu ya Asiriya anabwera nao anthu ochokera ku Babiloni, ndi ku Kuta, ndi ku Ava, ndi ku Hamati, ndi ku Sefaravaimu, nawakhalitsa m'mizinda ya Samariya, m'malo mwa ana a Israele; nakhala iwo eni ake a Samariya, nakhala m'mizinda mwake.


Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi Simisai mlembi, analemba kalata kwa mfumu Arita-kisereksesi, wakutsutsana naye Yerusalemu motere:


Nthawi yomweyi anawadzera Tatenai kazembe tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setari-Bozenai, ndi anzao, nanena nao motere, Anakulamulirani inu ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?


Zolembedwa m'kalata amene Tatenai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setari-Bozenai, ndi anzake Afarisikai, okhala tsidya lino la mtsinje, anatumiza kwa Dariusi mfumu,


Tsono iwe, Tatenai, kazembe wa tsidya lija la mtsinjewo, Setari-Bozenai, ndi anzanu Afarisikai, okhala tsidya lija la mtsinje, muzikhala kutali;


Nanena iye pamaso pa abale ake ndi ankhondo a ku Samariya, nati, Alikuchitanji Ayuda ofookawa? Adzimangire linga kodi? Adzapereka nsembe kodi? Adzatsiriza tsiku limodzi kodi? Adzakometsanso miyala ya ku miunda yotenthedwa?


Masiku ajawo, pokhala Ahasuwero pa mpando wa ufumu wake uli m'chinyumba cha ku Susa,


ndi mfumu aike oyang'anira m'maiko onse a ufumu wake, kuti asonkhanitse anamwali onse okongola m'chinyumba cha ku Susa, m'nyumba ya akazi; awasunge Hegai mdindo wa mfumu wosungira akazi, nawapatse zowayeretsa;


Masomphenya ovuta aonetsedwa kwa ine; wogula malonda wonyenga amangonyenga, ndi wofunkha amangofunkha. Kwera Elamu iwe; zunguniza Mediya iwe; kuusa moyo kwake konse ndakutonthoza.


ndi mafumu onse a Zimiri, ndi mafumu onse a Elamu, ndi mafumu onse a ku Mediya,


Mau a Yehova amene anafika kwa Yeremiya mneneri, onena za Elamu poyamba kulamulira Zedekiya mfumu ya Yuda, kuti,


Elamu ali komwe ndi gulu lake lonse lozinga manda ake; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga; amene anatsikira osadulidwa kunsi kwake kwa dziko, amene anaopsetsa m'dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.


Ndipo ndinaona m'masomphenya; tsono kunali, pakuwaona ine ndinali mu Susa, m'nyumba ya mfumu, ndiwo m'dziko la Elamu; ndinaona m'masomphenya kuti ndinali kumtsinje Ulai.


Aparti ndi Amedi, ndi Aelamu, ndi iwo akukhala mu Mesopotamiya, mu Yudeya, ndiponso mu Kapadokiya, mu Ponto, ndi mu Asiya;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa