Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 4:16 - Buku Lopatulika

16 Tili kudziwitsa mfumu kuti ukamangidwa mzindawu, nakatsirizidwa malinga ake, simudzakhala nalo gawo tsidya lino la mtsinjewo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Tili kudziwitsa mfumu kuti ukamangidwa mudziwu, nakatsirizidwa malinga ake, simudzakhala nalo gawo tsidya lino la mtsinjewo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Tikukudziŵitsani inu amfumu kuti ngati mzinda umenewu aumanganso ndi kutsirizanso makoma ake, ndiye kuti inuyo simudzatha kumalamulirabe m'chigawo cha Patsidya pa Yufuratecho.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Tsono tikukudziwitsani amfumu kuti ngati mzinda umenewu umangidwanso ndi makoma ake nʼkutsirizidwanso ndiye kuti inu simudzalamuliranso chigawo cha patsidya pa Yufurate.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 4:16
5 Mawu Ofanana  

Davide anakanthanso Hadadezere, mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba, pomuka iye kukadzitengeranso ufumu wake ku chimtsinje cha Yufurate.


Pakuti analamulira dziko lonse lili tsidya lino la Yufurate, kuyambira ku Tifisa kufikira ku Gaza, inde mafumu onse a ku tsidya lino la Yufurate; nakhala ndi mtendere kozungulira konseko.


kuti afunefune m'buku la chikumbutso la makolo anu; momwemo mudzapeza m'buku la chikumbutso, ndi kudziwa kuti mzinda uwu ndi mzinda wopanduka, ndi wosowetsa mafumu, ndi maiko; ndi kuti amadziyendera m'menemo kuyambira kale lomwe; ndicho chifukwa chakuti anapasula mzinda uwu.


Mfumu nibweza mau kwa Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi kwa Simisai mlembi, ndi kwa anzao otsala okhala mu Samariya, ndi otsala tsidya lino la mtsinjewo, Moni, ndi nthawi yakuti.


Panalinso mafumu amphamvu mu Yerusalemu amene anachita ufumu tsidya lija lonse la mtsinje, ndipo anthu anawapatsa msonkho, thangata, ndi msonkho wa m'njira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa