Ezara 4:10 - Buku Lopatulika10 ndi amitundu otsala amene, Osinapara wamkulu ndi womveka adawatenga mikoli, nawakhalitsa m'mizinda ya Samariya, ndi m'dziko lotsala tsidya lino la mtsinje wa Yufurate. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 ndi amitundu otsala amene, Osinapara wamkulu ndi womveka adawatenga mikoli, nawakhalitsa m'mudzi wa Samariya, ndi m'dziko lotsala tsidya lino la mtsinje wa Yufurate. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Enanso ndi mitundu ina imene Osinapara, wamkulu ndi womveka uja, adaisamutsa ndi kuikhazika m'mizinda ya Samariya ndi kwinanso m'madera a m'chigawo chimene chili Patsidya pa Yufurate.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 ndi mitundu ina imene mkulu wolemekezeka, Osanipara anayisamutsa ndi kuyikhazika mʼmizinda ya Samariya ndi mʼmadera ena apatsidya la Yufurate. Onani mutuwo |
Ndipo tsono, Mulungu wathu, ndinu Mulungu wamkulu, ndi wamphamvu, ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo, asachepe pamaso panu mavuto athu onse amene anatigwera ife, ndi mafumu athu, akulu athu, ndi ansembe athu, ndi aneneri athu, ndi makolo athu, ndi anthu anu onse, kuyambira masiku a mafumu a Asiriya, mpaka lero lino.