Ezara 3:8 - Buku Lopatulika8 Chaka chachiwiri tsono chakufika iwo kunyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, mwezi wachiwiri, Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ao otsala, ansembe ndi Alevi, ndi onse ochokera kundende kudza ku Yerusalemu, anayamba, naika Alevi a zaka makumi awiri ndi mphambu, ayang'anire ntchito ya nyumba ya Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Chaka chachiwiri tsono chakufika iwo kunyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, mwezi wachiwiri, Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ao otsala, ansembe ndi Alevi, ndi onse ochokera kundende kudza ku Yerusalemu, anayamba, naika Alevi a zaka makumi awiri ndi mphambu, ayang'anire ntchito ya nyumba ya Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Tsono chaka chachiŵiri atabwera ku Yerusalemu, ku mabwinja kumene kunali Nyumba ya Mulungu yakale, mwezi wachiŵiri, Zerubabele mwana wa Sealatiele ndiponso Yesuwa mwana wa Yozadaki, adayambapo ntchito pamodzi ndi abale ao otsala, ansembe ndi Alevi, ndi onse amene anali atabwera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo. Adasankha Alevi kuyambira anthu a zaka makumi aŵiri zakubadwa ndi opitirirapo, kuti aziyang'anira ntchito yomanga Nyumba ya Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Tsono mu chaka chachiwiri atabwera ku Yerusalemu, ku malo akale a Nyumba ya Yehova, mwezi wachiwiri Zerubabeli mwana wa Sealatieli, Yesuwa mwana wa Yozadaki pamodzi ndi abale awo onse, ansembe, Alevi ndi onse amene anabwera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo, anayamba kugwira ntchito. Iwo anasankha Alevi a zaka zoyambira makumi awiri kuti aziyangʼanira ntchito ya kumanga Nyumba ya Yehova. Onani mutuwo |