Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 3:7 - Buku Lopatulika

7 Anaperekanso ndalama kwa amisiri a miyala, ndi a mitengo; ndi chakudya, ndi chakumwa, ndi mafuta, kwa a ku Sidoni, ndi a ku Tiro, kuti atenge mikungudza ku Lebanoni, kufika nayo ku nyanja ku Yopa, monga adawalola Kirusi mfumu ya Persiya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Anaperekanso ndalama kwa amisiri a miyala, ndi a mitengo; ndi chakudya, ndi chakumwa, ndi mafuta, kwa a ku Sidoni, ndi a ku Tiro, kuti atenge mikungudza ku Lebanoni, kufika nayo ku nyanja ku Yopa, monga adawalola Kirusi mfumu ya Persiya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tsono anthu adapereka ndalama kwa amisiri osema miyala ndi kwa amisiri a matabwa. Adatumiza chakudya, zakumwa ndi mafuta kwa anthu a ku Sidoni ndi ku Tiro, kuti azigulira mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni. Mitengoyo adafika nayo ku nyanja mpaka ku mzinda wa Yopa. Zonsezi ankazichita potsata chilolezo cha Kirusi, mfumu ya ku Persiya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ndipo anapereka ndalama kwa amisiri a miyala ndi kwa amisiri a matabwa, ndi chakudya, chakumwa ndi mafuta kwa anthu a ku Sidoni ndi a ku Turo, kuti abweretse mitengo ya mkungudza pa nyanja kuchokera ku Lebanoni mpaka ku Yopa. Zonsezi anachita malinga ndi chilolezo chimene analandira kuchokera kwa Koresi, mfumu ya Peresiya.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 3:7
20 Mawu Ofanana  

Ndipo Hiramu mfumu ya Tiro anatumiza mithenga kwa Davide ndi mitengo yamkungudza, ndi amisiri a matabwa, ndi omanga nyumba; iwo nammangira Davide nyumba.


Ndipo tsono, lamulirani kuti anditemere mitengo yamkungudza ku Lebanoni, ndipo akapolo anga adzakhala ndi akapolo anu, ndipo ndidzakupatsani mphotho ya akapolo anu monga mudzanena; popeza mudziwa kuti pakati pa ife palibe mmisiri wakudziwa kutema mitengo ngati anthu a ku Sidoni.


Ndipo pakuona kuti ndalama zidachuluka m'bokosimo, anakwerako mlembi wa mfumu, ndi mkulu wa ansembe, nazimanga m'matumba, naziyesa ndalama zopereka m'nyumba ya Yehova.


Koma sanapangire nyumba ya Yehova mbale zasiliva, mbano, mbale zowazira, malipenga, zotengera zilizonse zagolide, kapena zotengera zilizonse zasiliva, kuzipanga ndi ndalama adabwera nazo kunyumba ya Yehova;


Ndipo anazipereka m'dzanja la antchito oikidwa ayang'anire nyumba ya Yehova; ndi iwo anazipereka kwa antchito akuchita m'nyumba ya Yehova kukonza ndi kulimbitsa nyumbayi;


Chiyambire tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri anapereka nsembe zopsereza kwa Yehova; koma sanamange maziko a Kachisi wa Yehova.


Yuda ndi dziko la Israele anagulana nawe malonda, anagula malonda ako ndi tirigu wa ku Miniti, ndi zozuna, ndi uchi, ndi mafuta, ndi mafuta amankhwala.


Koma Yona ananyamuka kuti athawire ku Tarisisi, kuzemba Yehova; ndipo anatsikira ku Yopa, napezako chombo chomuka ku Tarisisi, napereka ndalama zake, natsikira m'menemo, kuti apite nao ku Tarisisi kuzemba Yehova.


Koma Herode anaipidwa nao a ku Tiro ndi Sidoni; ndipo anamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m'mene adakopa Blasito mdindo wa mfumu, anapempha mtendere, popeza dziko lao linapeza zakudya zochokera ku dziko la mfumu.


Koma mu Yopa munali wophunzira dzina lake Tabita, ndilo kunena Dorika; mkazi ameneyo anadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo zimene anazichita.


Ndipo popeza Lida ndi pafupi pa Yopa, m'mene anamva ophunzirawo kuti Petro anali pomwepo, anamtumizira anthu awiri, namdandaulira, Musachedwa mudze kwa ife.


Ndipo kunali, kuti anakhala iye mu Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa