Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 3:6 - Buku Lopatulika

6 Chiyambire tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri anapereka nsembe zopsereza kwa Yehova; koma sanamange maziko a Kachisi wa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Chiyambire tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri anapereka nsembe zopsereza kwa Yehova; koma sanamange maziko a Kachisi wa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Kuyambira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanunchiŵiri, adayamba kupereka nsembe zopserezazi kwa Chauta. Koma maziko a Nyumba ya Mulungu anali asanamangidwebe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Kuyambira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri, iwo anayambanso kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova, ngakhale kuti maziko a Nyumba ya Yehova anali asanamangidwe.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 3:6
6 Mawu Ofanana  

atatero anaperekanso nsembe yopsereza yosalekeza, ndi za pokhala mwezi, ndi za nyengo zoikika zonse za Yehova zopatulika, ndi za munthu yense wopereka nsembe yaufulu kwa Yehova mwaufulu.


Anaperekanso ndalama kwa amisiri a miyala, ndi a mitengo; ndi chakudya, ndi chakumwa, ndi mafuta, kwa a ku Sidoni, ndi a ku Tiro, kuti atenge mikungudza ku Lebanoni, kufika nayo ku nyanja ku Yopa, monga adawalola Kirusi mfumu ya Persiya.


Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzipumula, ndiko chikumbutso cha kuliza malipenga, msonkhano wopatulika.


Musamagwira ntchito ya masiku ena; mubwere nayo nsembe yamoto ya Yehova.


Ndipo mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena; likukhalireni inu tsiku lakuliza malipenga.


Pamenepo muzipereka nsembe yopsereza ya fungo lokoma kwa Yehova; ng'ombe imodzi yamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi opanda chilema;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa