Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 3:2 - Buku Lopatulika

2 Nanyamuka Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ake ansembe, ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi abale ake, namanga guwa la nsembe la Mulungu wa Israele, kuperekapo nsembe zopsereza, monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose munthu wa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Nanyamuka Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ake ansembe, ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi abale ake, namanga guwa la nsembe la Mulungu wa Israele, kuperekapo nsembe zopsereza, monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose munthu wa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Pamenepo Yesuwa, mwana wa Zadoki, ndi ansembe anzake, pamodzi ndi Zerubabele, mwana wa Sealatiele, ndi abale ake, adayamba kumanga guwa la Mulungu wa Aisraele. Adafuna kuti aziperekapo nsembe zopsereza, monga adalembera m'buku la malamulo a Mose, munthu wa Mulungu uja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Kenaka Yesuwa mwana wa Yozadaki ndi ansembe anzake pamodzi ndi Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi abale ake anayamba kumanga guwa lansembe la Mulungu wa Israeli. Anatero pofuna kuti aziperekapo nsembe zopsereza monga analembera mʼbuku la Mose, munthu wa Mulungu uja.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 3:2
33 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.


Kunena za Mose munthu wa Mulunguyo, ana ake anatchulidwa mwa fuko la Levi.


Ndi mwana wa Yekoniya: Asiri, Sealatiele mwana wake,


Ndi ana a Pedaya: Zerubabele ndi Simei; ndi ana a Zerubabele: Mesulamu, ndi Hananiya; ndipo Selomiti ndiye mlongo wao,


Koma ndinasankha Yerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israele.


Ndipo anapeza mwa ana a ansembe odzitengera akazi achilendo, ndiwo a ana a Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ake Maaseiya, ndi Eliyezere, ndi Yaribu, ndi Gedaliya.


Ndi a ana a Imeri: Hanani ndi Zebadiya.


Ndi a ana a Harimu: Maaseiya, ndi Eliya, ndi Semaya, ndi Yehiyele, ndi Uziya.


Ndi a ana a Pasuri: Eliyoenai, Maaseiya, Ismaele, Netanele, Yozabadi, ndi Elasa.


ndiwo amene adadza ndi Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Seraya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu, Baana. Kuwerenga kwa amuna a anthu a Israele ndiko:


Chaka chachiwiri tsono chakufika iwo kunyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, mwezi wachiwiri, Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ao otsala, ansembe ndi Alevi, ndi onse ochokera kundende kudza ku Yerusalemu, anayamba, naika Alevi a zaka makumi awiri ndi mphambu, ayang'anire ntchito ya nyumba ya Yehova.


Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ananyamuka, nayamba kumanga nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu, anali pamodzi nao aneneri a Mulungu akuwathandiza.


Ndipo ansembe ndi Alevi amene anakwera ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa, ndi awa: Seraya, Yeremiya, Ezara,


Ndi Alevi ndiwo Yesuwa, Binuyi, Kadimiyele, Serebiya, Yuda, ndi Mataniya; iye ndi abale ake amatsogolera mayamiko.


koma anasankha fuko la Yuda, Phiri la Ziyoni limene analikonda.


Ndipo upange guwa la nsembe la mtengo wakasiya, utali wake mikono isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu, guwa la nsembelo likhale laphwamphwa, ndi msinkhu wake mikono itatu.


Chaka chachiwiri cha mfumu Dariusi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri kwa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kuti,


Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi otsala onse a anthu, anamvera mau a Yehova Mulungu wao, ndi mau a Hagai mneneri, monga Yehova Mulungu wao adamtuma; ndipo anthu anaopa pamaso pa Yehova.


Ndipo Yehova anautsa mzimu wa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi mzimu wa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi mzimu wa otsala onse a anthu, ndipo anadza nagwira ntchito m'nyumba ya Yehova wa makamu, Mulungu wao,


Nena ndi Zerubabele chiwanga cha Yuda, kuti, Ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi;


Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzakutenga, Zerubabele mtumiki wanga, mwana wa Sealatiele, ati Yehova, ndi kuika iwe ngati mphete yosindikizira; pakuti ndakusankha, ati Yehova wa makamu.


Pamenepo anandionetsa Yoswa mkulu wa ansembe alikuima pamaso pa mthenga wa Yehova, ndi Satana alikuima padzanja lake lamanja, atsutsana naye.


Tamvera tsono, Yoswa mkulu wa ansembe, iwe ndi anzako akukhala pansi pamaso pako; pakuti iwo ndiwo chizindikiro; pakuti taonani, ndidzafikitsa mtumiki wanga, ndiye Mphukira.


ndipo utenge siliva ndi golide, nupange akorona, nuwaike pamutu pa Yoswa mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe;


Uza ana a Israele, nuti nao, Muzisamalira kubwera nacho kwa Ine chopereka changa, chakudya changa cha nsembe zanga zamoto, cha fungo lokoma, pa nyengo yake yoikika.


mwana wa Yohanani, mwana wa Resa, mwana wa Zerubabele, mwana wa Sealatiele, mwana wa Neri,


Pamenepo Gideoni anammangira Yehova guwa la nsembe pomwepo; nalitcha Yehova-ndiye-mtendere; likali mu Ofura wa Aabiyezere ndi pano pomwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa