Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 10:8 - Buku Lopatulika

8 ndi kuti aliyense wosafikako atapita masiku atatu, monga mwa uphungu wa akalonga ndi akulu, chuma chake chonse chidzaonongeka konse, ndipo iye adzachotsedwa kumsonkhano wa iwo otengedwa ndende.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 ndi kuti aliyense wosafikako atapita masiku atatu, monga mwa uphungu wa akalonga ndi akulu, chuma chake chonse chidzaonongeka konse, ndipo iye adzachotsedwa kumsonkhano wa iwo otengedwa ndende.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Adanena kuti, “Wina aliyense akapanda kufika asanathe masiku atatu, ndiye kuti potsata lamulo la atsogoleri ndi la akulu, adzayenera kumlanda katundu wake yense, ndipo adzachotsedwe m'gulu la anthu obwerako ku ukapolo aja.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ananena kuti wina aliyense amene saonekera pakutha pa masiku atatu, adzalandidwa katundu wake, potsata malangizo a nduna ndi akuluakulu, ndipo adzachotsedwa mʼgulu la anthu obwerako ku ukapolo.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 10:8
14 Mawu Ofanana  

Nabukitsa iwo mau mwa Yuda ndi Yerusalemu kwa ana onse otengedwa ndende, kuti azisonkhana ku Yerusalemu;


Ndipo anasonkhana ku Yerusalemu amuna onse a Yuda ndi Benjamini asanapite masiku atatu, ndiwo mwezi wachisanu ndi chinai, tsiku la makumi awiri a mwezi; nakhala pansi anthu onse m'khwalala pakhomo pa nyumba ya Mulungu, alikunjenjemera chifukwa cha mlandu uwu, ndi chifukwa cha mvulayi.


Ndipo aliyense wosachita lamulo la Mulungu wako, ndi lamulo la mfumu, mlandu umtsutse msanga, ngakhale kumupha, kapena kumpirikitsa m'dziko, kapena kumlanda chuma chake, kapena kummanga m'kaidi.


Koma wina wa ana a Yehoyada, mwana wa Eliyasibu mkulu wa ansembe, anali mkamwini wa Sanibalati Muhoroni; chifukwa chake ndinampirikitsa kumchotsa kwa ine.


Ndipo kunali, atamva chilamulocho, anasiyanitsa pa Israele anthu osokonezeka onse.


Koma asachigulitse kapena kuchiombola chinthu choperekedwa chiperekere kwa Mulungu, chimene munthu achipereka chiperekere kwa Yehova, chotengako ku zonse ali nazo, ngakhale munthu, kapena nyama, kapena munda wakewake; chilichonse choperekedwa chiperekere kwa Mulungu nchopatulika kwambiri.


Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.


Adzakutulutsani m'masunagoge, koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.


Izi ananena atate wake ndi amake, chifukwa anaopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu aliyense adzamvomereza Iye kuti ndiye Khristu, akhale woletsedwa m'sunagoge.


Anayankha nati kwa iye, Wabadwa iwe konse m'zoipa, ndipo iwe utiphunzitse ife kodi? Ndipo anamtaya kunja.


koma akunja awaweruza Mulungu? Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.


Koma siliva yense, ndi golide yense, ndi zotengera za mkuwa ndi chitsulo zikhala chopatulikira Yehova; zilowe m'mosungira chuma cha Yehova.


Nati ana a Israele, Ndani iye mwa mafuko onse a Israele amene sanakwere kudza kumsonkhano kwa Yehova? Pakuti panali lumbiro lalikulu pa iye wosakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa, ndi kuti, Aphedwe ndithu.


Natenga ng'ombe ziwiri nazidula nthulinthuli, nazitumiza m'malire monse mwa Israele, ndi dzanja la mithenga, nati, Amene sakudza pambuyo pa Saulo ndi pa Samuele, adzatero nazo ng'ombe zake. Ndipo kuopsa kwa Yehova kunawagwera anthu, natuluka ngati munthu mmodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa