Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 1:8 - Buku Lopatulika

8 zomwezi Kirusi mfumu ya ku Persiya anazitulutsa ndi dzanja la Mitiredati wosunga chumayo, naziwerengera Sezibazara kalonga wa Ayuda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 zomwezi Kirusi mfumu ya ku Persiya anazitulutsa ndi dzanja la Mitiredati wosunga chumayo, naziwerengera Sezibazara kalonga wa Ayuda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Kirusi, mfumu ya ku Persiya, idazitulutsa zimenezi nkuzipereka kwa Metiredati, msungachuma wake, amene adaziŵerenga pamaso pa Sesibazara, nduna yaikulu ya ku dziko la Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Koresi, mfumu ya ku Perisiya inatulutsa ziwiyazi ndi kuzipereka kwa Miteridati, msungichuma amene anaziwerenga pamaso pa Sesibazara nduna yayikulu ya dziko la Yuda.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 1:8
10 Mawu Ofanana  

Zipangizo zonse zagolide ndi zasiliva ndizo zikwi zisanu ndi mazana anai. Izi zonse Sezibazara anakwera nazo, pokwera andende aja kuchokera ku Babiloni kunka ku Yerusalemu.


ndiwo amene adadza ndi Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Seraya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu, Baana. Kuwerenga kwa amuna a anthu a Israele ndiko:


Ndiponso zipangizo za golide ndi siliva za nyumba ya Mulungu, anazitulutsa Nebukadinezara mu Kachisi anali ku Yerusalemu, ndi kubwera nazo ku Kachisi wa ku Babiloni, izizo Kirusi mfumu anazitulutsa mu Kachisi wa ku Babiloni, nazipereka kwa munthu dzina lake Sezibazara, amene anamuika akhale kazembe;


Pamenepo anadza Sezibazara yemweyo namanga maziko a nyumba ya Mulungu ili mu Yerusalemu; ndipo kuyambira pomwepo kufikira tsopano ilinkumangidwa, koma siinatsirizike.


Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ananyamuka, nayamba kumanga nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu, anali pamodzi nao aneneri a Mulungu akuwathandiza.


Ndipo Ine ndiweruza Beli mu Babiloni, ndipo ndidzatulutsa m'kamwa mwake chomwe wachimeza; ndipo amitundu sadzasonkhaniranso konse kwa iye; inde, khoma la Babiloni lidzagwa.


Chaka chachiwiri cha mfumu Dariusi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri kwa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kuti,


Ndipo Yehova anautsa mzimu wa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi mzimu wa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi mzimu wa otsala onse a anthu, ndipo anadza nagwira ntchito m'nyumba ya Yehova wa makamu, Mulungu wao,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa