Ezara 1:7 - Buku Lopatulika7 Kirusi mfumu anatulutsanso zipangizo za nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara adazitulutsa mu Yerusalemu, ndi kuziika m'nyumba ya milungu yake; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Kirusi mfumu anatulutsanso zipangizo za nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara adazitulutsa m'Yerusalemu, ndi kuziika m'nyumba ya milungu yake; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Nayenso mfumu Kirusi adatulutsa ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta zimene Nebukadinezara adaazitenga kuzichotsa ku Yerusalemu, kudzaziika m'nyumba ya milungu yake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Nayenso mfumu Koresi anatulutsa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara anazitenga kuzichotsa ku Yerusalemu ndi kuziyika mʼnyumba ya milungu yake. Onani mutuwo |
Ndiponso zipangizo za golide ndi siliva za nyumba ya Mulungu, anazitulutsa Nebukadinezara mu Kachisi anali ku Yerusalemu, ndi kubwera nazo ku Kachisi wa ku Babiloni, izizo Kirusi mfumu anazitulutsa mu Kachisi wa ku Babiloni, nazipereka kwa munthu dzina lake Sezibazara, amene anamuika akhale kazembe;
koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu aang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitire ulemu.