Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 1:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo aliyense wotsala pamalo paliponse agonerapo iye, anthu a kumalo kwake amthandize ndi siliva, ndi golide, ndi zoweta, ndi chuma, pamodzi ndi nsembe yaufulu ya kwa nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo aliyense wotsala pamalo paliponse agonerapo iye, anthu a kumalo kwake amthandize ndi siliva, ndi golide, ndi zoweta, ndi chuma, pamodzi ndi nsembe yaufulu ya kwa nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Motero kulikonse kumene anthu otsalawo amakhala, athandizidwe ndi eni dzikolo. Aŵapatse siliva ndi golide, katundu ndi ziŵeto, ndi zopereka zaufulu zoti akapereke ku Nyumba ya Mulungu, imene ili ku Yerusalemu.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndipo kumalo kulikonse kumene otsalawo akukhala, athandizidwe ndi eni dzikolo powapatsa siliva, golide, katundu ndi ziweto ndi zopereka za ufulu zoti akapereke ku Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Ezara 1:4
15 Mawu Ofanana  

Ndidziwanso, Mulungu wanga, kuti muyesa mtima, nimukondwera nako kuongoka. Koma ine, ndi mtima wanga woongoka ndapereka zonsezi mwaufulu; ndipo tsopano ndaona mokondwera anthu anu okhala pompano, napereka kwa Inu mwaufulu.


Ndiponso popeza ndikondwera nayo nyumba ya Mulungu wanga, chuma changachanga cha golide ndi siliva ndili nacho ndichipereka kunyumba ya Mulungu wanga, moonjezera ndi zonse ndazikonzeratu nyumba yopatulikayo;


Ndipo anthu anakondwera popeza anapereka mwaufulu; pakuti ndi mtima wangwiro anapereka mwaufulu kwa Yehova; mfumu Davide yemwe anakondwera ndi chimwemwe chachikulu.


Ndipo Kore mwana wa Imina Mlevi, wa kuchipata cha kum'mawa, anayang'anira zopereka zaufulu za Mulungu, kugawira nsembe zokweza za Yehova, ndi zopatulika kwambiri.


Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Mulungu wake akhale naye, akwere kunka ku Yerusalemu, ndiwo mu Yuda, nakaimange nyumba ya Yehova Mulungu wa Israele; Iye ndiye Mulungu wokhala mu Yerusalemu.


Pamenepo ananyamuka akulu a nyumba za makolo a Yuda ndi Benjamini, ndi ansembe, ndi Alevi, ndiwo onse amene Mulungu adawautsira mzimu wao akwere kukamanga nyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu.


Yehova Mulungu wa Israele, Inu ndinu wolungama, popeza tinatsala opulumuka monga lero lino; taonani, tili pamaso panu m'kupalamula kwathu; pakuti palibe wakuima pamaso panu chifukwa cha ichi.


Amuna ndi akazi onse a ana a Israele amene mitima yao inawafunitsa eni kubwera nazo za ku ntchito yonse imene Yehova analamula ipangike ndi dzanja la Mose, anabwera nacho chopereka chaufulu, kuchipereka kwa Yehova.


Otsala adzabwera, otsala a Yakobo, kwa Mulungu wamphamvu.


Ndipo zitapita zaka zambiri ndinadza kutengera mtundu wanga zachifundo, ndi zopereka;


Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Khristu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa