Akapolo onse a mfumu ndi anthu a m'maiko a mfumu adziwa kuti aliyense, ngakhale wamwamuna kapena wamkazi, akalowa kwa mfumu kubwalo la m'katimo wosaitanidwa, lamulo la pa iye ndi limodzi, ndilo kuti amuphe, akapanda mfumu kumloza ndi ndodo yachifumu yagolide kuti akhale ndi moyo; koma ine sanandiitane ndilowe kwa mfumu masiku awa makumi atatu.