Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Estere 8:3 - Buku Lopatulika

3 Nanenanso Estere pamaso pa mfumu, nagwa ku mapazi ake, nalira misozi, nampembedza kuti achotse choipacho cha Hamani wa ku Agagi, ndi chiwembu adachipangira Ayuda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Nanenanso Estere pamaso pa mfumu, nagwa ku mapazi ake, nalira misozi, nampembedza kuti achotse choipacho cha Hamani wa ku Agagi, ndi chiwembu adachipangira Ayuda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Estere anayankhulanso ndi mfumu ndipo anadzigwetsa pa mapazi ake. Uku akulira iye anapempha mfumu kuti iletse choyipa, makamaka chiwembu chimene Hamani Mwagagi anakonza kuti awononge a Yuda.

Onani mutuwo Koperani




Estere 8:3
10 Mawu Ofanana  

Ndipo pofika kwa munthu wa Mulungu kuphiri anamgwira mapazi. Ndipo Gehazi anayandikira kuti amkankhe; koma munthu wa Mulungu anati, Umleke, pakuti mtima wake ulikumuwawa; ndipo Yehova wandibisira osandiuza ichi.


Zitatha izi, mfumu Ahasuwero anamkuza Hamani mwana wa Hamedata, wa ku Agagi, namkweza, naika mpando wake upose akalonga onse okhala naye.


pakuti tagulitsidwa; ine ndi anthu a mtundu wanga, kuti ationonge, atiphe, natipulule. Koma tikadagulitsidwa tikhale akapolo ndi adzakazi, ndikadakhala chete; chinkana wosautsa sakadatha kubwezera kusowa kwa mfumu.


Ndipo mfumu inavula mphete yake adailanda kwa Hamani, naipereka kwa Mordekai. Ndi Estere anaika Mordekai akhale woyang'anira nyumba ya Hamani.


Ndipo mfumu inaloza Estere ndi ndodo yachifumu yagolide. Nanyamuka Estere, naima pamaso pa mfumu.


Ndipo Hezekiya analoza nkhope yake kukhoma, napemphera kwa Yehova, nati,


inde, analimbana ndi wamthenga nampambana; analira, nampembedza Iye; anampeza Iye ku Betele, ndi kumeneko Iye analankhula ndi ife;


Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


Ndipo atagwadira pa mapazi ake anati, Pa ine, mbuye wanga, pa ine pakhale uchimowo; ndipo mulole mdzakazi wanu alankhule m'makutu anu, nimumvere mau a mdzakazi wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa