Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Estere 7:9 - Buku Lopatulika

9 Nati Haribona wina wa adindo okhala pamaso pa mfumu, Taonaninso, mtengowo msinkhu wake mikono makumi asanu, umene Hamani anaupangira Mordekai wonenera mfumu zokoma, uimiritsidwa m'nyumba ya Hamani. Niti mfumu, Mpachike pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Nati Haribona wina wa adindo okhala pamaso pa mfumu, Taonaninso, mtengowo msinkhu wake mikono makumi asanu, umene Hamani anaupangira Mordekai wonenera mfumu zokoma, uimiritsidwa m'nyumba ya Hamani. Niti mfumu, Mpachike pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Haribona, mmodzi wa adindo ofulidwa amene ankatumikira mfumu anati, “Mtanda wotalika mamita 23 uli mʼnyumba ya Hamani. Mtandawu, Hamani anapangira Mordekai, uja amene anapulumutsa mfumu ku chiwembu.” Mfumu inati, “Mpachikeni pamenepo!”

Onani mutuwo Koperani




Estere 7:9
20 Mawu Ofanana  

Koma anakweza maso ake kuzenera, nati, Ali ndi ine ndani? Ndani? Nampenyererako adindo awiri kapena atatu.


Tsiku lachisanu ndi chiwiri, pokondwera mtima wa mfumu ndi vinyo, iye anauza Mehumani, Bizita, Haribona, Bigita, ndi Abagita, Zetara, ndi Karikasi, adindo asanu ndi awiriwo akutumikira pamaso pa mfumu Ahasuwero,


Pamenepo Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse ananena naye, Apange mtengo, msinkhu wake mikono makumi asanu, ndi mawa mukanene nayo mfumu kuti ampachike Mordekai pamenepo; nimulowe pamodzi ndi mfumu kumadyerero wokondwera. Ndipo ichi chidakomera Hamani, napangitsa anthu mtengowo.


Akali chilankhulire naye, anafika adindo a mfumu, nafulumira kumtenga Hamani kunka naye kumadyerero adawakonzera Estere.


Napeza mudalembedwa kuti Mordekai adawulula za Bigitana ndi Teresi, awiri a adindo a mfumu osunga pakhomo, amene adayesa kumthira manja mfumu Ahasuwero.


Pamenepo mfumu Ahasuwero anati kwa mkazi wamkulu Estere, ndi kwa Mordekai Myuda, Taonani, ndampatsa Estere nyumba ya Hamani, ndi iyeyu anampachika pamtanda, chifukwa anatulutsa dzanja lake pa Ayuda.


Ndipo mfumu inati azichita motero, nalamulira mu Susa, napachikidwa ana aamuna khumi a Hamani.


koma pofika mlanduwo kwa mfumu, iye adalamula polemba kalata kuti chiwembu choipa cha Hamani adachipangira Ayuda chimbwerere mwini; ndi kuti iye ndi ana ake aamuna apachikidwe pamtengo.


Oipa agwe pamodzi m'maukonde ao, kufikira nditapitirira ine.


Chimgwere modzidzimutsa chionongeko; ndipo ukonde wake umene anautcha umkole yekha mwini, agwemo, naonongeke m'mwemo.


Ha? M'kamphindi ayesedwa bwinja; athedwa konse ndi zoopsa.


Ndipo italamulira mfumu, anabwera nao amuna aja adamneneza Daniele, nawaponya m'dzenje la mikango, iwowa, ana ao, ndi akazi ao; ndipo asanafike pansi pa dzenje mikango inawaposa mphamvu, niphwanya mafupa ao onse.


Akulu onse a ufumuwo, ndi akazembe ndi akalonga, mandoda, ndi ziwanga, anapangana kukhazika lemba lachifumu, ndi kuikapo choletsa cholimba, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango.


Potero Davide anathamanga naima pa Mfilistiyo, nagwira lupanga lake, nalisolola m'chimake, namtsiriza nadula nalo mutu wake. Ndipo pakuona Afilisti kuti chiwinda chao chidafa, anathawa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa