Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Estere 7:3 - Buku Lopatulika

3 Nayankha mkazi wamkulu Estere, nati, Ngati mwandikomera mtima, mfumu, ndipo chikakomera mfumu, andilekere moyo wanga pa kupempha kwanga, ndi wa anthu a mtundu wanga pa pempho langa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Nayankha mkazi wamkulu Estere, nati, Ngati mwandikomera mtima, mfumu, ndipo chikakomera mfumu, andilekere moyo wanga pa kupempha kwanga, ndi wa anthu a mtundu wanga pa pempho langa;

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Kenaka mfumukazi Estere anayankha kuti, “Ngati mwandikomera mtima, inu mfumu, ndipo ngati chingakukomereni mfumu, pempho ndi chokhumba changa ndi ichi, mulole kuti ine ndi abale anga tisungidwe tonse ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani




Estere 7:3
9 Mawu Ofanana  

Pamenepo anyamata ake anati kwa iye, Taonani, tidamva ife kuti mafumu a nyumba ya Israele ndi mafumu achifundo; tiyeni tivale chiguduli m'chuuno mwathu, ndi zingwe pamitu pathu, titulukire kwa mfumu ya Israele, kapena adzakusungirani moyo.


Ndipo anabwerezanso kutuma mtsogoleri wachitatu ndi makumi asanu ake. Nakwera mtsogoleri wachitatuyo, nadzagwada ndi maondo ake pamaso pa Eliya, nampembedza, nanena naye, Munthu wa Mulungu inu, ndikupemphani, moyo wanga ndi moyo wa anyamata anu makumi asanu awa akhale a mtengo wake pamaso panu.


Anampatsanso chitsanzo cha lamulo lolembedwa adalibukitsa mu Susa, kuwaononga, achionetse kwa Estere, ndi kumfotokozera, ndi kumlangiza alowe kwa mfumu, kumpembedza, ndi kupempherera anthu ake kwa iye.


ngati mfumu indikomera mtima, ngatinso chakomera mfumu kupereka pempho langa ndi kuchita chofuna ine, adze mfumu ndi Hamani ku madyerero ndidzawakonzera; ndipo mawa ndidzachita monga yanena mfumu.


Ninyamuka mfumu mu mkwiyo wake ku madyerero a vinyo, nimka kumunda wa maluwa wa kuchinyumba; koma Hamani anatsalira kudzipempherera moyo kwa mkazi wamkulu Estere; popeza anapenya kuti mfumu inatsimikiza mtima kumchitira choipa.


Nati, Chikakomera mfumu, ndipo ngati yandikomera mtima, ndi kumuyenera mfumu, ngatinso ndimchititsa kaso, alembe makalata kusintha mau a chiwembu cha Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, amene adawalembera kuononga Ayuda okhala m'maiko onse a mfumu;


Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.


pamenepo uziti kwa iwo, Ndinagwa ndi pembedzero langa pamaso pa mfumu, kuti asandibwezerenso kunyumba ya Yonatani ndifere komweko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa