Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Estere 5:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo Estere anati, Chikakomera mfumu, adze mfumu ndi Hamani lero ku madyerero ndinawakonzera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Estere anati, Chikakomera mfumu, adze mfumu ndi Hamani lero ku madyerero ndinawakonzera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndipo Estere anayankha kuti, “Ngati chingakukomereni, mfumu, mubwere lero pamodzi ndi Hamani kuphwando limene ndakonzera inu mfumu.”

Onani mutuwo Koperani




Estere 5:4
10 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anati, Usendere nayo kwa ine, ndidye nyama ya mwana wanga, kuti moyo wanga ukudalitse iwe. Ndipo anasendera nayo kwa iye, nadya iye; ndipo anamtengera vinyo, namwa iye.


ndiponso muziti, Ndiponso, taonani, kapolo wanu Yakobo ali pambuyo pathu. Pakuti anati, Ndidzampembedzera iye ndi mphatso imene ipita patsogolo panga, pambuyo pake ndidzaona nkhope yake; kapena adzandilandira ine.


Vasiti yemwe, mkazi wamkulu, anakonzera akazi madyerero m'nyumba yachifumu ya mfumu Ahasuwero.


Amtokoma anatuluka ofulumizidwa ndi mau a mfumu, ndi lamulo linabukitsidwa m'chinyumba cha ku Susa; ndipo mfumu ndi Hamani anakhala pansi kumwa; koma mzinda wa Susa unadodoma.


Ninena naye mfumu, Mufunanji, Estere mkazi wamkulu? Pempho lanu nchiyani? Lidzaperekedwa kwa inu, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.


Niti mfumu, Mumfulumize Hamani, achitike mau a Estere. Nidza mfumu ndi Hamani ku madyerero adawakonzera Estere.


ngati mfumu indikomera mtima, ngatinso chakomera mfumu kupereka pempho langa ndi kuchita chofuna ine, adze mfumu ndi Hamani ku madyerero ndidzawakonzera; ndipo mawa ndidzachita monga yanena mfumu.


Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa; adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa.


Chitsiru chivumbulutsa mkwiyo wake wonse; koma wanzeru auletsa nautontholetsa.


Abale, musakhale ana m'chidziwitso, koma m'choipa khalani makanda, koma m'chidziwitso akulu misinkhu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa